Pitani ku nkhani yake

APRIL 11, 2018
KAZAKHSTAN

A Teymur Akhmedov Anatulutsidwa M’ndende ya ku Kazakhstan pa 4 April, 2018

A Teymur Akhmedov Anatulutsidwa M’ndende ya ku Kazakhstan pa 4 April, 2018

Pulezidenti wa dziko la Kazakhstan, a Nursultan Nazarbayev, anakhululukira a Teymur Akhmedov, ndipo anamasulidwa m’ndende pa 4 April, 2018. Pa 27 March, 2018, akuluakulu a boma analola kuti M’bale Akhmedov akapangidwe opaleshoni mwamsanga ku chipatala cha Almaty komwe akulandira thandizo ndipo panopa akupezako bwino.

M’bale Akhmedov, ali ndi zaka 62 ndipo anakhala m’ndende kuyambira pa 18 January, 2017 chifukwa cha chikhulupiriro chake. Panopa m’baleyu ndi wosangalala kwambiri kuti alinso ndi banja lake.

Ndife osangalala kuti Yehova anapulumutsa mtumiki wake.—2 Samueli 22:2