Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Kodi Baibulo Lingandithandize Bwanji?—Gawo 1: Kuganizira Mozama Mfundo za M’baibulo

Kodi Baibulo Lingandithandize Bwanji?—Gawo 1: Kuganizira Mozama Mfundo za M’baibulo

 “Nthawi zambiri ndikafuna kuwerenga Baibulo, ndimangogwa ulesi chifukwa ndimaona kuti n’chibuku chachikulu.”​—Briana.

 Ngati nanunso mumamva choncho, nkhaniyi ingakuthandizeni.

 N’chifukwa chiyani kuwerenga Baibulo n’kofunika?

 Kodi mumaona kuti kuwerenga Baibulo ndi kosasangalatsa? Ngati ndi choncho, si inu nokha. Mwina mumaona kuti Baibulo ndi buku lalikulu, la masamba ambiri koma lopanda zithunzi moti simungaliyerekezere ndi mmene mumasangalalira mukamaonera TV kapena mavidiyo.

 Koma tiyerekeze kuti mwaona chikwama cha ndalama chomwe chikuoneka kuti ndi chakale, kodi simungakhale ndi chidwi kuti muone zimene zili mkatimo?

 Baibulo lili ngati chikwama choterocho. Mumapezeka mfundo zanzeru zomwe zingakuthandizeni. Lingakuthandizeni pa nkhani zotsatirazi:

  •   Kuti muzisankha zochita mwanzeru

  •   Kuti muzigwirizana ndi makolo anu

  •   Kuti mupeze anzanu abwino

  •   Kuti muchepetse nkhawa

 Koma kodi zingatheke kuti buku lakaleli likhale lothandiza masiku ano? Inde, tikutero chifukwa “malemba onse anauziridwa ndi Mulungu.” (2 Timoteyo 3:16) Zimenezi zikusonyeza kuti malangizo a m’Baibulo anachokera kwa munthu wodalirika kwambiri.

Baibulo lili ngati chikwama chokhala ndi mfundo zamtengo wapatali komanso zopatsa nzeru

 Ndingatani kuti kuwerenga Baibulo kuzindisangalatsa?

 Choyamba, muziliwerenga kuchokera kumayambiriro mpaka kumapeto. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kumvetsa uthenga wonse wa m’Baibulo. Koma pali njira zambiri zothandiza powerenga Baibulo. Mwachitsanzo, mungatsatire njira izi:

  •    Mungawerenge mabuku onse 66 a m’Baibulo kuyambira Genesis mpaka Chivumbulutso.

  •    Mukhozanso kumawerenga Baibulo motsatira nthawi imene zinthu zinazake zinachitika.

 Zimene Zingakuthandizeni: Werengani Zakumapeto 21 mu Baibulo la Dziko Latsopano kuti muone zochitika zikuluzikulu m’moyo wa Yesu ali padziko lapansi.

 Chachiwiri, muzisankha nkhani yogwirizana ndi mavuto amene mukukumana nawo. Mwachitsanzo:

  •    Ngati mukufuna kupeza anzanu odalirika, werengani nkhani ya Yonatani ndi Davide. (1 Samueli chaputala 18 mpaka 20) Kenako gwiritsani ntchito tsamba la pawebusaiti yathu lakuti, “Zimene Mungachite Kuti Mupeze Anzanu Odalirika” kuti muone mfundo zimene zingakuthandizeni.

  •    Ngati mukufuna kuti musamagonje mukakumana ndi mayesero, werengani nkhani ya Yosefe kuti muone zimene anachita atakumana ndi mayesero. (Genesis chaputala 39) Kenako gwiritsani ntchito tsamba la pawebusaiti yathu lakuti, “Zimene Mungachite Mukakumana ndi Mayesero? . . . Yosefe​—Gawo 1” komanso nkhani yakuti, “Anaimbidwa Mlandu Womunamizira, Yosefe​—Gawo 2” kuti muone mfundo zimene zingakuthandizeni.

  •    Ngati mukufuna kudziwa mmene pemphero lingakuthandizireni, werengani nkhani ya Nehemiya. (Nehemiya, chaputala 2) Kenako gwiritsani ntchito tsamba la pawebusaiti yathu lakuti, “Mulungu Anayankha Pemphero Lake” kuti muone mfundo zimene zingakuthandizeni.

 Zimene Zingakuthandizeni: Mukamawerenga Baibulo, muzionetsetsa kuti mwakhala pamalo opanda phokoso kuti musasokonezedwe.

 Chachitatu, muzisankha nkhani inayake kapena salimo linalake, kenako muziganizira mmene nkhaniyo ingakuthandizireni. Mukamaliza kuwerenga muzidzifunsa kuti:

  •    N’chifukwa chiyani Yehova analola kuti zimenezi zilembedwe m’Baibulo?

  •    Kodi zimenezi zikundiphunzitsa chiyani za Yehova komanso mmene amachitira zinthu?

  •    Kodi mfundo zomwe ndaphunzirazi ndingazigwiritse ntchito bwanji pa moyo wanga?

 Zimene Zingakuthandizeni: Konzani ndandanda yabwino yoti muziwerenga Baibulo tsiku lililonse ndipo lembani tsiku limene mukufuna kuyamba kuwerengako.