Pitani ku nkhani yake

Kodi Baibulo Limaphunzitsa Kuti Munthu Akamwalira Amakabadwanso Kwinakwake?

Kodi Baibulo Limaphunzitsa Kuti Munthu Akamwalira Amakabadwanso Kwinakwake?

Yankho la m’Baibulo

 Ayi siliphunzitsa zimenezi. Ndipotu m’Baibulo mulibe mawu alionse osonyeza kuti munthu akamwalira amakabadwanso kwinakwake. Chikhulupiriro choti munthu akamwalira amakabadwanso kwinakwake chinachokera ku chiphunzitso choti munthu akamwalira mzimu wake suufa. a Komabe, Baibulo likamanena za mzimu limatanthauza munthu wamoyo. (Genesis 2:7; Ezekieli 18:4) Choncho munthu akamwalira sapitiriza kukhalanso ndi moyo chifukwa moyo wake umakhala kuti wathera pompo.​—Genesis 3:19; Mlaliki 9:5, 6.

Kodi mfundo yoti munthu akafa amakabadwanso kwina ndi yosiyana bwanji ndi mfundo yoti akufa adzauka?

 Zimene Baibulo limanena zoti akufa adzauka sizigwirizana ndi zimene anthu amanena kuti munthu ali ndi mzimu umene umapitirizabe kukhala ndi moyo munthuyo akamwalira. Pa nkhani ya kuuka kwa akufa, Mulungu adzagwiritsa ntchito mphamvu zake kuchititsa anthu amene anamwalira kukhalanso ndi moyo. (Mateyu 22:23, 29; Machitidwe 24:15) Kuukitsidwa kwa akufa kumatipatsa chiyembekezo chabwino chodzakhala ndi moyo wosatha m’dziko lapansi latsopano.—2 Petulo 3:13; Chivumbulutso 21:3, 4.

Maganizo olakwika pa mfundo yoti munthu akafa amakabadwanso kwina komanso zimene Baibulo limanena

 Maganizo olakwika: Baibulo limanena kuti mneneri Eliya atafa anabadwanso n’kukhala Yohane Mbatizi.

 Zoona zake: Mulungu analosera kuti: “Ndidzakutumizirani mneneri Eliya,” ndipo Yesu anasonyeza kuti Yohane Mbatizi ndi amene anakwaniritsa ulosi wonena za iyeyo. (Malaki 4:5, 6; Mateyu 11:13, 14) Komabe, izi sizikutanthauza kuti Eliya atamwalira anabadwanso n’kukhala Yohane Mbatizi. Yohane ananena yekha kuti iyeyo sanali Eliya. (Yohane 1:21) M’malo kwake, Yohane anagwira ntchito yofanana ndi imene Eliya ankagwira, yomwe inali yolengeza uthenga wa Mulungu wouza anthu kuti alape. (1 Mafumu 18:36, 37; Mateyu 3:1) Komanso Yohane anasonyeza kuti anali “ndi mphamvu ngati za Eliya.”—Luka 1:13-17.

 Maganizo olakwika: Baibulo likamanena za “kubadwanso” limatanthauza kuti munthu akamwalira amakabadwanso kwinakwake.

 Zoona zake: Baibulo limasonyeza kuti munthu amabadwanso adakali ndi moyo ndipo umakhala umboni woti wadzozedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. (Yohane 1:12, 13) Munthu samabadwanso chifukwa cha zimene ankachita m’moyo wakale, koma chifukwa chakuti Mulungu wamudalitsa. Anthu oterewa amayembekezera kudzalandira mphoto yapadera m’tsogolo.​—Yohane 3:3; 1 Petulo 1:3, 4.

a Anthu a ku Babulo ndi amene anayambitsa chikhulupiriro chakuti munthu akamwalira mzimu wake umapitirizabe kukhala ndi moyo, komanso chakuti munthu akafa amakabadwanso kwinakwake. Kenako, akatswiri a nzeru za anthu a ku India anayambitsa chiphunzitso chotchedwa Karma. Buku lina linanena kuti Karma ndi “lamulo lomwe limanena kuti zimene munthu akuchita m’moyo uno, zimadzakhala ndi zotsatira zake m’moyo wotsatira.”​—Britannica Encyclopedia of World Religions, tsamba  913.