Pitani ku nkhani yake

Kodi Mulungu Angandikhululukire Machimo Anga?

Kodi Mulungu Angandikhululukire Machimo Anga?

Yankho la m’Baibulo

 Inde, Mulungu akhoza kukukhululukirani machimo anu ngati mutalapa. Baibulo limanena kuti Mulungu ndi “wokonzeka kukhululuka” ndiponso “amakhululuka ndi mtima wonse.” (Nehemiya 9:17; Salimo 86:5; Yesaya 55:7) Mulungu akatikhululukira, amakhala ngati ‘wafafaniza’ kapena kufufuta machimo athu. (Machitidwe 3:19) Akakhululuka zimakhala ngati waiwala machimo a munthu. N’chifukwa chake ananena kuti: “Machimo awo sindidzawakumbukiranso.” (Yeremiya 31:34) Zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu sakumbutsanso machimo athu n’cholinga choti atilange.

 Komabe, Mulungu akamakhululukira anthu zolakwa zawo, sizisonyeza kuti ndi wolekerera zinthu. Sikuti amasiya kutsatira mfundo zake zachilungamo n’cholinga choti akhululukire munthu. N’chifukwa chake, nthawi zina sakhululukira munthu amene sakufuna kulapa.​—Yoswa 24:19, 20.

Zimene mungachite kuti Mulungu akukhululukireni

  1.   Muyenera kuvomereza kuti mwachita zinthu zimene Mulungu amadana nazo. M’malo mongoganiza kuti mwalakwira anthu amene mwawakhumudwitsawo, ndibwino kumakumbukiranso kuti mwalakwira Mulungu.​—Salimo 51:1, 4; Machitidwe 24:16.

  2.   Muuzeni Mulungu zimene mwachitazo kudzera m’pemphero.​—Salimo 32:5; 1 Yohane 1:9.

  3.   Muzidzimvera chisoni chifukwa cha zimene mwachitazo. Kuchita zimenezi ‘n’kogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu’ ndipo kungakuthandizeni kuti musinthe n’kuyamba kuchita zabwino. (2 Akorinto 7:10) Zimenezi zikuphatikizaponso kumva chisoni chifukwa cha zimene munachita, zomwe zinachititsa kuti muchite tchimo.​—Mateyu 5:27, 28.

  4.   Muyenera “kutembenuka” kapena kuti kusiyiratu zoipa zimene munachitazo. (Machitidwe 3:19) Zimenezi zikutanthauza kuti muyenera kupewa kubwerezanso zoipazo komanso muyenera kusintha zochita ndiponso kaganizidwe kanu.​—Aefeso 4:23, 24.

  5.   Popeza zimene munachitazo zinakhudzanso anthu ena, muyenera kukonza mavuto amene abwera chifukwa cha zochita zanuzo. (Mateyu 5:23, 24; 2 Akorinto 7:11) Muyenera kupepesa anthu omwe munawalakwira komanso amene anakhudzidwa ndi zochita zanuzo.​—Luka 19:7-10.

  6.   Pemphani Mulungu kuti akukhululukireni pogwiritsa ntchito nsembe ya Yesu. (Aefeso 1:7) Ndiye kuti Mulungu achite zimenezi, nanunso muyenera kumakhululukira anthu amene akulakwirani.​—Mateyu 6:14, 15.

  7.   Ngati mwachita tchimo lalikulu kwambiri, mungachite bwino kuuza munthu woyenerera amene angakuthandizeni komanso kukupemphererani kwa Mulungu kuti akukhululukireni.​—Yakobo 5:14-16.

Maganizo olakwika amene anthu ena amakhala nawo

 “Ndachimwa kwambiri moti Mulungu sangandikhululukire.”

Mulungu anakhululukira Davide atachita tchimo la chigololo ndiponso kupha munthu

 Ngati titayesetsa kuchita zimene takambirana pamwambazi, Mulungu akhoza kutikhululukira ngakhale zitakhala kuti tachita tchimo lalikulu. Mulungu akhozanso kukhululukira munthu amene wakhala akuchita machimo mobwerezabwereza.​—Miyambo 24:16; Yesaya 1:18.

 Mwachitsanzo, Davide yemwe anali mfumu ya Isiraeli, anachita chigololo komanso kupha munthu. Ngakhale anachita machimo akuluakuluwa, Mulungu anamukhululukira. (2 Samueli 12:7-13) Komanso, Mulungu anakhululukira mtumwi Paulo ngakhale kuti ankadziona kuti ndi munthu woipa kwambiri. (1 Timoteyo 1:15, 16) Mulungu akanakhululukiranso Ayuda omwe anapha Yesu, pokhapokha Ayudawo akanasintha n’kumachita zimene iye amafuna.​—Machitidwe 3:15, 19.

 “Ndikangoulula machimo anga kwa wansembe kapena m’busa, ndiye kuti basi machimo anga akhululukidwa.”

 Palibe munthu amene Mulungu anamupatsa udindo woti azikhululuka machimo. Ngakhale kuti kuuza munthu wina tchimo limene tachita kungathandize kuti tisiye kuchita tchimolo, Mulungu ndi amene amakhululukira machimo osati munthu.​—Aefeso 4:32; 1 Yohane 1:7, 9.

 Ngati zimenezi zili zoona, ndiye n’chifukwa chiyani Yesu anauza atumwi kuti: “Mukakhululukira munthu amene wachita tchimo, ndiye kuti Mulungu wamukhululukira kale. Koma mukapanda kukhululukira munthu amene wachita tchimo, ndiye kuti Mulungu sanamukhululukire”? (Yohane 20:23) Apa Yesu ankasonyeza kuti atumwiwo adzapatsidwa udindo waukulu kwambiri akadzalandira mzimu woyera.​—Yohane 20:22.

 Atumwi analandira mzimu woyerawu m’chaka cha 33 C.E. (Machitidwe 2:1-4) Mwachitsanzo mtumwi Petulo anagwiritsa ntchito mzimu woyera poweruza Hananiya ndi Safira ndipo iye ankadziwa zochita zawo zachinyengo. Chiweruzo chimene anawapatsa chinasonyeza kuti machimo awo sangakhululukidwe.​—Machitidwe 5:1-11.

 Mphatso ya mzimu woyera, yomwe analandirayo, inasiya kugwira ntchito atumwiwo atatha onse kufa.(1 Akorinto 13:8-10) Zimenezi zikusonyezeratu kuti masiku ano n’zosatheka kuti munthu akhale ndi udindo wokhululukira machimo a munthu wina.