Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 24

Yehova Ni Wokonzeka Kukhululuka

Yehova Ni Wokonzeka Kukhululuka

“Inu Yehova ndinu Mulungu wabwino ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka. Kukoma mtima kosatha kumene mumawasonyeza onse oitana pa inu ndi kwakukulu.” —SAL. 86:5.

NYIMBO 42 Pemphelo la Mtumiki wa Mulungu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Malinga na Mlaliki 7:20, ni mfundo yoona iti imene Mfumu Solomo anakamba?

 MFUMU Solomo analemba kuti: “Palibe munthu wolungama padziko lapansi amene amacita zabwino zokha-zokha osacimwa.” (Mlal. 7:20) Mfundo imeneyi ni yoona. Tonsefe ndife ocimwa. (1 Yoh. 1:8) Conco, timafuna kuti Mulungu komanso anthu azitikhululukila.

2. Mumamva bwanji mnzanu wa pamtima akakukhululukilani?

2 Mosakaikila, mukumbukila nthawi imene munakhumudwitsa mnzanu wa pamtima. Pofuna kukonza zinthu komanso ubwenzi wanu, munapepesa mocokela pansi pamtima. Kodi munamva bwanji mnzanuyo atakukhululukilani na mtima wonse? Munamva bwino ndipo munakondwela, si conco kodi?

3. Kodi tikambilane mafunso ati m’nkhani ino?

3 Timafuna kuti Yehova akhale bwenzi lathu la pamtima. Koma nthawi zina, tingakambe kapena kucita zinthu zomukhumudwitsa. N’cifukwa ciyani tingakhale otsimikiza kuti Yehova ni wokonzeka kutikhululukila macimo athu? N’cifukwa ciyani kukhululuka kwa Yehova n’kwapadela poyelekezela na mmene anthufe timakhululukilana? Ndipo cothela, ndani amapindula na cikhululuko ca Mulungu?

YEHOVA NI WOKONZEKA KUKHULULUKA

4. N’ciyani citipangitsa kukhala otsimikiza kuti Yehova ni wokonzeka kukhululuka?

4 Mawu a Mulungu amatitsimikizila kuti Yehova ni wokonzeka kukhululuka. Pamene Yehova anadzifotokoza kwa Mose pa Phili la Sinai, iye kupitila mwa mngelo anati: “Yehova, Yehova, Mulungu wacifundo ndi wacisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi coonadi. Wosungila mibadwo masauzande kukoma mtima kosatha, wokhululukila zolakwa ndi macimo.” (Eks. 34:6, 7) Yehova ni Mulungu wokoma mtima komanso wacifundo, amene nthawi zonse ni wokonzeka kukhululukila ocimwa amene alapa.—Neh. 9:17; Sal. 86:15.

Yehova amadziŵa bwino zonse zimene zaticitikila pa umoyo kuti tikhale mtundu wa munthu amene tili (Onani ndime 5)

5. Malinga n’kunena kwa Salimo 103:13, 14, kodi Yehova amacita nafe motani cifukwa cotidziŵa bwino?

5 Popeza Yehova ndiye anatilenga, iye amadziŵa zonse zokhudza ife. Tangoganizani! Iye amadziŵa zonse zokhudza munthu aliyense padzikoli. (Sal. 139:15-17) Conco, amaona ucimo wonse umene tinatengela kwa makolo athu. Kuwonjezela apo, iye amadziŵa zonse zinacitika mu umoyo wathu zimene zinaumba umunthu wathu. Kodi kuwadziŵa bwino anthu mwa njila imeneyi kumasonkhezela Yehova kucita ciyani? Kumamusonkhezela kucita nawo mwacifundo.—Sal. 78:39; ŵelengani Salimo 103:13, 14.

6. Kodi Yehova anaonetsa bwanji kuti ni wofunitsitsa kutikhululukila?

6 Yehova anaonetsa kuti ni wofunitsitsa kutikhululukila. Iye amadziŵa kuti cifukwa ca zocita za munthu woyamba, Adamu, tonsefe tinalandila tembelelo la ucimo na imfa. (Aroma 5:12) Panalibe njila ina iliyonse yodziwombola tokha ku tembelelo limeneli, kapena kuwombola munthu wina. (Sal. 49:7-9) Koma Mulungu wathu wacikondi anaonetsa cifundo na kukonza zakuti adzatiwombole. Kodi iye anacita ciyani? Monga mmene Yohane 3:16 imakambila, Yehova anapeleka Mwana wake wobadwa yekha kuti adzatifele. (Mat. 20:28; Aroma 5:19) Yesu anavutika mpaka kufa m’malo mwa ife, kuti amasule aliyense wokhulupilila mwa iye. (Aheb. 2:9) Cinamuŵaŵa kwambili Yehova kuona Mwana wake wokondeka akufa imfa yoŵaŵa komanso yocititsa manyazi. Kukamba zoona, ngati Yehova sanali kufuna kutikhululukila sakanatumiza Mwana wake kuti adzatifele.

7. Ni zitsanzo za m’Baibo ziti za anthu amene Yehova anawakhululukila na mtima wonse?

7 M’Baibo, muli zitsanzo za anthu ambili amene Yehova anawakhululukila na mtima wonse. (Aef. 4:32) Kodi ndani amabwela m’maganizo mwanu? Mwina mumaganizila za Mfumu Manase. Munthu woipa ameneyu anacimwila Yehova m’njila zambili. Iye ndiye anali patsogolo kulimbikitsa kulambila konyenga. Anapha ana ake na kuwapeleka nsembe ku milungu yacikunja. Anafika ngakhale poika cifanizilo cosema mkati mwenimweni mwa kacisi woyela wa Yehova. Pokamba za iye, Baibo imati: “Iye anacita zinthu zambili zoipa pamaso pa Yehova ndiponso zomukwiyitsa.” (2 Mbiri 33:2-7) Koma Manase atalapa mocokela pansi pamtima, Yehova anamukhululukila na mtima wonse. Ndipo Mulungu anamubwezeletsa pa ufumu wake. (2 Mbiri 33:12, 13) Mwina mungaganizilenso za Mfumu Davide, amene anacimwila Yehova mwa kucita macimo akulu-akulu, omwe anaphatikizapo cigololo na kupha munthu. Ngakhale n’telo, Davide atalapa mocokela pansi pamtima, Yehova anamukhululukila. (2 Sam. 12:9, 10, 13, 14) Inde, tingakhale otsimikiza kuti Yehova amafunitsitsa kutikhululukila. Ndipo monga tionele, iye amakhululuka mwapadela kwambili poyelekezela na mmene anthufe timakhululukilana.

YEHOVA AMAKHULULUKA MWAPADELA KWAMBILI

8. Kodi Yehova amatha bwanji kukhululuka mwacilungamo?

8 Yehova ni “Woweluza wa dziko lonse lapansi.” (Gen. 18:25) Woweluza wabwino ayenela kuwadziŵa bwino malamulo. Ndipo Yehova ni woweluza wotelo, cifukwa iye amapanganso malamulo. (Yes. 33:22) Kupatulapo Yehova, palibe aliyense amene amadziŵa bwino coyenela komanso cosayenela. Kodi woweluza wabwino ayenela kuganizila ciyani? Ayenela kuona mfundo zonse zokhudza nkhani asanapeleke ciweluzo cake. Pambali imeneyi, Yehova ndiye woweluza wabwino koposa.

9. Kodi Yehova amaganizila ciyani pofuna kukhululukila munthu?

9 Kusiyana na mmene anthu amaweluzila, Yehova nthawi zonse amadziŵa bwino zonse zokhudza nkhani iliyonse asanaweluze. (Gen. 18:20, 21; Sal. 90:8) Iye sapeleka ciweluzo motengela zimene anthu amaona kapena kumva. Amamvetsa bwino kwambili cifukwa cake munthu amacita zinthu mwa njila ina yake. Amaganizila cibadwa ca munthuyo, mmene analeledwela, kumene anakulila, kaganizidwe kake, komanso mmene amamvela. Yehova amadziŵanso zili mu mtima mwa munthu. Iye amadziŵa bwino zolinga komanso zikhumbo za munthu aliyense. Palibe cobisika kwa Yehova. (Aheb. 4:13) Conco, Yehova akakhululukila munthu amakhala kuti wapenda zonse zokhudza munthuyo.

Yehova ni wacilungamo, alibe tsankho, ndipo sangapatsidwe ciphuphu (Onani ndime 10)

10. N’cifukwa ciyani tingati ziweluzo za Yehova nthawi zonse zimakhala za cilungamo? (Deuteronomo 32:4)

10 Ziweluzo za Yehova nthawi zonse zimakhala zacilungamo. Iye alibe tsankho. Kukhululuka kwake sikudalila maonekedwe a munthu, cuma, kudziŵika, kapena maluso ake. (1 Sam. 16:7; Yak. 2:1-4) Palibe angakakamize Yehova kucita zina zake kapena kum’patsa ciphuphu. (2 Mbiri 19:7) Iye sapeleka zigamulo cifukwa cothedwa nzelu, kapena kukondela. (Eks. 34:7) Mosakaika konse, Yehova ni woweluza wabwino koposa cifukwa amamvetsetsa kwambili, komanso ni wozindikila.—Ŵelengani Deuteronomo 32:4.

11. N’ciyani capadela na kukhululuka kwa Yehova?

11 Olemba Malemba Acihebeli anazindikila kuti Yehova amakhululuka mwapadela kwambili. Nthawi zina polemba, iwo anali kuseŵenzetsa mawu amene buku lina linati mawuwo, “amakambidwa maka-maka pofuna kufotokoza mmene Mulungu amakhululukila munthu wocimwa. Ndipo mawuwo sakambidwa pofuna kuonetsa kukhululukilana kumene kumacitika pakati pa anthu.” Ni Yehova yekha amene ali na mphamvu zokhululukila mokwanila munthu wocimwa wolapa. Kodi pamakhala zotsatilapo zotani Yehova akatikhululukila?

12-13. (a) Kodi munthu amapindula bwanji akakhululukidwa na Yehova? (b) Kodi mapindu okhululukidwa na Yehova amakhalapo kwa utali wotani?

12 Tikavomeleza kuti Yehova anatikhululukila, timakondwela na “nyengo zotsitsimutsa,” ndipo timakhala na mtendele wamaganizo komanso cikumbumtima coyela. Cikhululuko cotelo ‘cimacokela kwa Yehova,’ osati kwa anthu. (Mac. 3:19) Yehova akatikhululukila, amakonzanso ubwenzi wathu ndipo zimakhala monga sitinacimwepo kumbuyoku.

13 Yehova akatikhululukila, sakatiimbanso mlandu kapena kutilanga pa chimo limenelo. (Yes. 43:25; Yer. 31:34) Yehova amatiikila ‘kutali zolakwa zathu monga mmene kum’mawa kulili kotalikilana na kumadzulo.’ * (Sal. 103:12) Tikaganizila mmene Yehova amatikhululukila mwapadela, timakhala oyamikila ndipo timakhudzika mtima. (Sal. 130:4) Koma kodi ndani angapindule na cikhululuko ca Yehova cimeneci?

KODI YEHOVA AMAKHULULUKILA NDANI?

14. Pofika pano, kodi taphunzila kuti Yehova amacita ciyani kuti apange cisankho cokhululukila munthu?

14 Monga taonela, Yehova pofuna kukhululukila munthu sayang’ana kukula kapena kucepa kwa chimo limene wacita. Cina, taphunzila kuti Yehova amaseŵenzetsa cidziŵitso cake monga Mlengi wathu, Wopanga Malamulo, komanso Woweluza akafuna kukhululukila munthu. Kodi amaganizila ciyani kuti acite izi?

15. Malinga na Luka 12:47, 48, kodi Yehova amaganizila mfundo iti asanakhululukile munthu?

15 Yehova pokhululukila munthu amaona ngati munthuyo anali kudziŵa kuti zimene anali kucita n’zoipa kapena ayi. Yesu anachula mfundo imeneyi momveka bwino pa Luka 12:47, 48. (Ŵelengani.) Munthu amene mwadala amakonzekela kuti acite coipa, pamene akudziŵa bwino kuti cimene akucitaco n’kucimwila Yehova, amacita chimo lalikulu. Munthu wotelo amakhala pa ciopsezo, cifukwa Yehova angasankhe kusam’khululukila. (Maliko 3:29; Yoh. 9:41) Koma tiyenela kuvomeleza kuti nthawi zina timadziŵa ndithu kuti zimene tinacita n’zoipa. Koma kodi pali ciyembekezo cakuti Yehova angatikhululukile? Inde! Izi zitifikitsa pa mfundo ina imene Yehova amaganizila.

Tingakhulupilile kuti Yehova adzatikhululukila tikalapa mocokela pansi pamtima (Onani ndime 16-17)

16. Kodi kulapa kutanthauza ciyani? Nanga n’cifukwa ciyani kulapa n’kofunika kuti Yehova atikhululukile?

16 Pofuna kukhululukila munthu, Yehova amaona ngati wocimwayo ni wolapadi mocokela pansi pamtima. Kodi kulapa kutanthauza ciyani? Kulapa kumatanthauza “kusintha kaganizidwe, kaonedwe ka zinthu, kapena kusintha zolinga.” Kuphatikizapo kudziimba mlandu komanso kudzimvela cisoni kwambili pa zoipa zimene anacita, kapena polephela kucita zoyenela. Munthu wolapa amadzimvela cisoni pa zoipa zimene anacita, komanso kufooka kwake kuuzimu kumene kunam’tsogolela kucita zoipazo. Kumbukilani kuti Mfumu Manase komanso Mfumu Davide, onse anacita macimo aakulu. Ngakhale n’telo, Yehova anawakhululukila cifukwa iwo analapa mocokela pansi pamtima. (1 Maf. 14:8) Inde, Yehova amafuna umboni wotsimikizila kuti munthu ni wolapa kuti am’khululukile. Koma kungodzimvela cabe cisoni pa macimo amene timacita, kapena chimo limene tacita si kokwanila. Tiyenela kucitapo kanthu. * Izi zitifikitsanso pa mfundo ina imene Yehova amaganizila.

17. Kodi kusintha kumatanthauza ciyani? Nanga n’cifukwa ciyani kusintha n’kofunika kuti tisabwelezenso macimo akale? (Yesaya 55:7)

17 Cina cofunika cimene Yehova amaona ni kusintha kwa munthu. Kusintha kumatanthauza “kutembenuka.” M’mawu ena, munthu ayenela kusintha umoyo wake mwa kuleka kucita zoipa, na kuyamba kucita zimene Yehova amafuna. (Ŵelengani Yesaya 55:7.) Munthuyo ayenela kusanduliza maganizo ake n’colinga cakuti aziona zinthu mmene Yehova amazionela. (Aroma 12:2; Aef. 4:23) Ayenela kuyesetsa kuleka khalidwe lake loipa, na kucotsa maganizo osayenela. (Akol. 3:7-10) Koma kuti Yehova atikhululukile na kutiyeletsa ku macimo athu, tiyenela kukhulupilila nsembe ya dipo la Khristu. Iye adzatikhululukila pogwilitsa nchito nsembe imeneyo, akaona kuti tayesetsa kusintha khalidwe lathu.—1 Yoh. 1:7.

MUZIKHULUPILILA KUTI YEHOVA ADZAKUKHULULUKILANI

18. Kodi taphunzila ciyani za cikhululuko ca Yehova?

18 Mwacidule, tiyeni tibweleze mfundo zazikulu zimene takambilana. Yehova ni wokonzeka kukhululuka kuposa aliyense m’cilengedwe conse. N’cifukwa ciyani takamba conco? Coyamba, iye nthawi zonse ni wokonzeka kukhululuka. Caciŵili, amatidziŵa bwino kwambili. Amadziŵa bwino cibadwa cathu, ndipo ndiye ali pamalo oyenela oona ngati ndife olapadi. Ndipo cacitatu, Yehova akakhululuka amafutilatu macimo athu, titelo kukamba kwake. Izi zimatithandiza kukhala na cikumbumtima coyela, komanso oyanjidwa na iye.

19. Ngakhale ndife opanda ungwilo ndipo tizicimwabe, n’cifukwa ciyani tingakhale acimwemwe?

19 Popeza ndife opanda ungwilo, tizicimwabe. Komabe, tingalimbikitsidwe na mawu a m’buku la Insight on the Scriptures voliyumu 2, tsamba 771, imene imati: “Yehova ni wacifundo, ndipo amadziŵa zifooko za atumiki ake. Conco, iwo sayenela kumva cisoni nthawi zonse akalakwa cifukwa ca kupanda ungwilo kumene anatengela. (Sal. 103:8-14; 130:3) Akayesetsa mmene angathele kuyenda m’njila za Mulungu, angakhale acimwemwe. (Afil 4:4-6; 1 Yoh. 3:19-22).” Iyi ni mfundo yolimbikitsa kwambili!

20. Tidzakambilana ciyani m’nkhani yotsatila?

20 Tiyamikila kwambili kuti Yehova ni wokonzeka kutikhululukila tikalapa macimo athu mocokela pansi pamtima. Koma kodi tingam’tengele bwanji Yehova pa nkhani yokhululuka? Kodi timafanana pa ciyani na Yehova pa nkhani yokhululuka? Nanga timasiyana m’njila ziti? N’cifukwa ciyani tiyenela kumvetsa kusiyana kumeneku? Nkhani yotsatila idzayankha mafunso amenewa.

NYIMBO 45 Kusinkha-sinkha kwa Mtima Wanga

^ M’mawu ake, Yehova amatitsimikizila kuti iye ni wokonzeka kukhululukila anthu ocimwa amene alapa. Koma nthawi zina, tingaone kuti sindife oyenela cikhululuko cake. M’nkhani ino, tikambilane cifukwa cake tingakhale otsimikiza kuti Mulungu wathu, nthawi zonse amakhala wokonzeka kutikhululukila tikalapadi macimo athu mocokela pansi pamtima.

^ KUFOTOKOZELA MAWU ENA: “Kulapa” kumatanthauza kusintha kaganizidwe, kophatikizapo kudzimvela cisoni pa zoipa zimene munthu anacita, kapena zimene analephela kucita. Kulapa kwenikweni kumabala zipatso zabwino mwa munthuyo, zimene ni kusintha umoyo wake.