Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MMENE ZOPELEKA ZANU ZIMAGWILILA NCHITO

Malo Amene Amalemekeza Mlangizi Wathu Wamkulu

Malo Amene Amalemekeza Mlangizi Wathu Wamkulu

JULY 1, 2023

 Yehova amakonda kuphunzitsa anthu ake. Kamba ka ico, gulu lake lakhazikitsa masukulu osiyana-siyana amene amathandiza ophunzila kukwanilitsa mautumiki awo. Imodzi ya masukuluwo ni Sukulu ya Alengezi a Ufumu. M’zaka zaposacedwa, gulu la Mulungu lakhala likuganizilanso kwambili za malo amene pamacitikila masukuluwa, osati cabe za maphunzilo amene ophunzila amalandila. Colinga cacikulu ni kufuna kukhala na malo abwino amene ophunzila komanso alangizi azicitilapo masukuluwa. Kodi zopeleka zanu zimatithandiza bwanji kukwanilitsa colinga cimeneci?

Ophunzila Ambili pa Malo Abwino Ophunzililapo

 Kwa zaka zambili, masukulu a zaumulungu akhala akucitikila mu Nyumba za Ufumu komanso m‘Mabwalo a Misonkhano. Nanga n’cifukwa ciyani takhala tikumanga kapena kukonzanso nyumba zina zimene zimagwilitsidwa nchito cabe pocita masukulu a zaumulungu? Onani zifukwa zitatu izi.

 Pakufunika anchito ambili. M’bale Christopher Mavor, wothandiza m’Komiti ya Utumiki ya Bungwe Lolamulila, anati: “Maofesi a nthambi atiuza kuti pakufunika anchito ambili m’gawo.Mwacitsanzo, mu 2019, ofesi ya nthambi ku Brazili inati pakufunika otsiliza maphunzilo a Sukulu ya Alengezi pafupifupi 7,600 kuti asamalile zofunika za m’gawo la nthambi yawo.” Nthambi ya ku United States inati pakufunika apainiya ambili amene angaphunzitse ena mocitila ulaliki wapoyela wa m’mizinda ikulu-ikulu, ulaliki wa padoko, komanso ulaliki wa ku ndende. Pakufunikanso abale ambili amene angatumikile mu Dipatimenti ya Mapulani na Mamangidwe (LDC) komanso m’Makomiti Okambilana na Acipatala (HLC). Otsiliza maphunzilo a Sukulu ya Alengezi angagwile bwino nchito zimenezi.

 Kuwonjezeka kwa ophunzila. Nthambi zambili zalandila mafomu oculuka a ofunsila kuloŵa Sukulu ya Alengezi kuposa ciŵelengelo ca anthu amene angakwanitse kuwaloŵetsa sukuluyi pali pano. Mwacitsanzo, m’caka cimodzi cabe, ofesi ya nthambi ku Brazil inalandila mafomu pafupifupi 2,500 a ofunsila kuloŵa Sukulu ya Alengezi. Koma cifukwa ca kucepekela kwa malo ocitilapo sukuluyi, ofesiyo inangotengapo ophunzila 950 cabe.

 Malo abwino okhala. Ophunzila akamacitila sukuluyi pa Nyumba ya Ufumu kapena pa Bwalo la Msonkhano, nthawi zambili amakhala kunyumba za abale na alongo. Makonzedwewa amagwila bwino nchito ku malo amene sikucitika makalasi ambili m’caka. Koma kumene kumacitika makalasi ambili, zingakhale zosatheka kuti ofalitsa asunge ophunzila kwa miyezi yambili m’caka. Conco nyumba zimakonzedwa pafupi na makalasi, ndipo nyumbazi anazikonzela ophunzila.

 Kumanga kalasi imodzi, nyumba za alangizi komanso za ophunzila 30, na zinthu zina zofunikila, kungaloŵetse ndalama madola mamiliyoni ambili a ku America, malinga na kumene amangidwila komanso zolowetsedwamo zina.

Zopezeka pa Malo a Sukulu

 Masukuluwa amakonzedwela kunja kwa mizinda ikulu-ikulu, ku malo opanda phokoso, komanso kumene mayendedwe si ovuta. Masukuluwa amamangidwila ku malo komwe kuli ofalitsa ambili amene angathandize kuti sukulu iziyenda bwino na kusamalila zimango komanso zipangizo za pa malopo.

 Pa malopo pamakhala malaibulale, malo oŵelengela, makompyuta, zipangizo zopulintila, na zipangizo zina. Kambili pamakhala cipinda codyela. Conco ophunzila na alangizi amadyela capamodzi. Pamakhalanso malo okwanila ocitila zolimbitsa thupi komanso zosangalatsa.

 Cipinda cophunzililamo cimakonzedwa mwapadela. “Tinafunsila ku Dipatimenti ya Masukulu a Zaumulungu kuti atithandize kupanga pulani ya zipinda zophunzililamo kuti malowo azikhala abwino kuphunzililamo,” anatelo Troy, amene amaseŵenzela ku Dipatimenti Yoona za Mapulani na Zomanga-manga pa Dziko Lonse ku Warwick, New York. Iye anapitiliza kuti: “Abale anatipatsa malangizo a kukula kwa zipindazo na mmene ziyenela kumangidwila, komanso mtundu wa malaiti, zokuzila mawu na zotambitsila mavidiyo zimene zingafunike.” Ponena za zokuzila mawu, Zoltán, amene ni mlangizi wa Sukulu ya Alengezi ku Hungary, anati: “Poyamba, tinalibe mamaikolofoni. Conco kambili tinali kufunika kumawakumbutsa ophunzila kuti akambe mokweza. Koma popeza lomba pa tebulo iliyonse pamakhala maikolofoni, vutolo linatha!”

“Alendo Apadela a Yehova”

 Kodi zimango zatsopanozi zawathandiza bwanji alangizi na ophunzila? Angela, amene analoŵa sukulu ya Alengezi ku Palm Coast, Florida, U.S.A anati: “Ni malo a bata kwambili. Zonse zinakonzedwa bwino, kuphatikizapo makalasi na zipinda zathu, kuti zitithandize kuika maganizo athu pa kuphunzila na kuŵelenga.” M’bale Csaba, amene ni mlangizi ku Hungary, amayamikila mwayi wodyela pamodzi na ophunzila. Iye anati pa nthawi yakudya, “ophunzila amamasuka kutifotokozela mmene zinthu zilili kwa iwo komanso zimene zinaŵacitikilapo. Izi zimatithandiza kuti tiwadziŵe bwino ophunzilawo. Zotulukapo zake n’zakuti timatha kuphunzitsa zinthu mogwilizana na zosoŵa zawo.”

 Ophunzila na alangizi amaona kuti malo a masukulu okonzedwa bwino amenewa ni dalitso locokela kwa “Mlangizi [wathu] Wamkulu,” Yehova. (Yesaya 30:20, 21) Mlongo wa ku Philippines amene analoŵapo Sukulu ya Alengezi pa malo amene anasinthidwa kukhala ocitilapo masukulu ananena kuti: “Malo a sukuluyi anatikumbutsa kuti si ndife ophunzila cabe, koma ndifenso alendo apadela a Yehova. Amafuna tizisangalala pamene tikuphunzila Mawu ake mozama.”

 Masukulu amamangidwa, kukonzedwanso, na kusamalidwa cifukwa ca zopeleka zanu, zimene ambili amapeleka kupitila pa donate.dan124.com. Zikomo kwambili cifukwa ca kuwolowa manja kwanu.

Pakhomo la sukulu, Palm Coast, Florida, ku U.S.A.

Cifanizilo ca kacisi wa m’nthawi ya Yesu, cipinda ca masukulu, ku Palm Coast, Florida, U.S.A.

Afika ku Sukulu ya Alengezi a Ufumu ku Brazil

Maphunzilo ali mkati ku Brazil

Afika ku Sukulu ya Alengezi a Ufumu ku Philippines

Akudyela capamodzi cakudya ca masana m’cipinda codyela ku Philippines