Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MMENE ZOPELEKA ZANU ZIMAGWILILA NCHITO

Zidindo Zimene Zimasintha Miyoyo ya Anthu

Zidindo Zimene Zimasintha Miyoyo ya Anthu

OCTOBER 1, 2021

 Nsanja ya Mlonda ya June 1, 1912 inati: “Mwacionekele anthu ambili amene amaŵelenga magazini athu, amadziŵako anthu ena akhungu. Ndipo angawatengeleko mabuku a akhungu aulele . . . . Mabuku amenewa a akhungu amapulintidwa m’zilembo zotumphukako pang’ono kuti akhungu azitha kuziŵelenga.” Nsanja imeneyi inapitiliza kuti: “Anthu ambili akhungu amayamikila kumva uthenga wa madalitso osaneneka amene tidzalandila padziko lapansi m’tsogolo.”

 Pamene mawuwa anali kulembedwa, panali pasanakhazikitsidwe kalembedwe kamodzi ka zilembo za akhungu m’Cizungu m’maiko osiyanasiyana. Ngakhale n’conco, ife Mboni za Yehova tinali titayamba kale kupanga mabuku a anthu akhungu ofotokoza coonadi ca m’Baibo. Ndipo tikali kupangabe! Lomba tili na mabuku a anthu akhungu m’zinenelo zoposa 50. Kodi amapangidwa bwanji?

Magulu a zidindo kuyambila pa cimodzi mpaka pa 6, zimaimila zilembo. Zidindozo zimayalidwa m’tumabokosi tokhala na mbali 6 m’bokosi iliyonse

Kupanga Mabuku a Anthu Akhungu

 Popanga mabuku a anthu akhungu, coyamba pamafunika kusintha mawu m’kuwaika m’zilembo za akhungu. M’bale Michael Millen wa m’dipatimenti ya Text Processing Services ku Patterson, New York anati: “Kumbuyoku, tinali kuseŵenzetsa pulogilamu ya pa kompyuta yopangidwa na anthu ena posintha mawu kuwaika m’zilembo za anthu akhungu, koma siinali kukwanitsa kusintha mawu a zinenelo zonse zimene tinali kufuna. Tsopano timaseŵenzetsa pulogilamu yochedwa Watchtower Translation System, imene imakwanitsa kulemba zilembo za anthu akhungu m’zinenelo zambili. Nikhulupilila palibe pulogilamu yofanana na imeneyi kwina kulikonse.”

 Mabuku a anthu akhungu amakhalanso na mawu ofotokozela zithunzi.Mwacitsanzo, cithunzi ca pacikuto ca buku la akhungu lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! anacifotokozela motele: “Mwamuna wayamba kuyenda pa njila yokhota-khota, imene m’mbali mwake muli maluŵa na mitengo yokongola komanso mapili.” M’bale Jamshed, amene ni mtumiki wothandiza komanso mpainiya wakhungu, anati: “Mawu ofotokozela zithunzi amenewa ni othandiza kwambili kwa ine.”

 Nchito yosintha mawu n’kuwaika m’zilembo za anthu akhungu ikatha, mafaelo amatumizidwa ku ofesi ya nthambi kuti akapange zofalitsa za anthu akhungu. Popanga mabuku a anthu akhungu, amagwilitsila nchito pepala lolimba kwambili limene silingawonongeke popangapo, kapena kupindika pambuyo pogwilitsila nchito mabukuwo kwa nthawi yaitali. Kenako, mapepalawo amaphatikizidwa pamodzi n’kukhala mabuku. Ndipo mabukuwo amatumizidwa ku mipingo mwa nthawi zonse, kapena pogwilitsila nchito positi ofesi imene ili na makonzedwe otumizila zinthu anthu akhungu kwaulele. Pakakhala pofunikila, maofesi a nthambi amapanga makonzedwe akuti zofalitsa zimenezi zitumizidwe mwamsanga, kuti abale na alongo akhungu kapena amene amavutikila kuona akhale na zofalitsa zoseŵenzetsa pa misonkhano ya mpingo.

 Nchito imeneyi imafuna nthawi yoculuka komanso ndalama zambili. Mwacitsanzo, nthawi imene makina athu opulintila mabuku a ku Wallkill, New York, amatenga popanga Mabaibo aŵili cabe a anthu akhungu, imafanana na nthawi imene makinawo amatenga popanga Mabaibo wamba 50,000. Ndalama zofunikila popanga Baibo imodzi ya Cizungu ya anthu akhungu yokhala na mavoliyumu 25, zimakhala zofanana na ndalama zofunikila popanga Mabaibo 123 a anthu amene si akhungu. a Zikuto cabe za mavoliyumu 25 a Baibo imodzi ya akhungu zimaloŵetsa ndalama zokwana madola 150 a ku America!

Baibulo la Dziko Latsopano la Cizungu la giledi 2 la anthu akhungu lili na mavoliyumu 25!

 Kodi anthu amene amathandiza popanda mabuku a anthu akhungu amamvela bwanji na nchito yawo? Mlongo Nadia, amene amatumikila pa ofesi ya nthambi ya South Africa anati: “Umoyo ni wovuta kwa abale na alongo athu amene ni akhungu kapena amene amavutikila kuona. Conco nimaona kuti ni mwayi kupanga zinthu zimene zimawathandiza. Ndipo n’zoonekelatu kuti Yehova amawakonda kwambili.”

Phunzilani Kuŵelenga Zilembo za Osaona

 Bwanji ngati munthu wakhungu sakwanitsa kuŵelenga zilembo za anthu osaona? Zaka zingapo zapitazo, tinatulutsa buku lakuti Phunzilani Kuŵelenga Zilembo za Osaona. Buku limeneli lili na mbali ziŵili, zilembo za anthu osaona komanso zilembo za anthu amene amakwanitsa kuona. Buku limeneli linakonzedwa m’njila yakuti munthu wakhungu komanso amene amakwanitsa kuona aziligwilitsila nchito pamodzi. Buku limeneli ni limodzi mwa zida zimene anthu akhungu amaseŵenzetsa polemba zilembo za osaona. Munthu wophunzila kuŵelenga zilembo za osaona, amaseŵenzetsa zida zimenezi podzilembela yekha cilembo ciliconse ca osaona. Akamacita zimenezi, wophunzilayo amatha kukumbukila cilembo ciliconse mosavuta na kucizindikila mwa kungocigwila.

“Nikayamba Kuŵelenga Sinifuna Kuleka”

 Kodi abale na alongo amene ni osaona kapena amene amavutikila kuona apindula bwanji na zofalitsa zimenezi? M’bale Ernst, wa ku Haiti, anali kupezeka pa misonkhano ya mpingo, koma analibe cofalitsa ciliconse ca anthu osaona. Conco iye anali kucita kuloŵeza zokakamba pa nkhani ya ophunzila imene wapatsidwa komanso popeleka ndemanga pa misonkhano. Iye anati: “Koma tsopano, nimakweza dzanja na kupeleka ndemanga nthawi iliyonse pa misonkhano. Nimamva kuti nikucitiladi limodzi zinthu na abale na alongo. Tonse tikulandila cakudya cauzimu cofanana!”

 M’bale Jan, ni mkulu wovutikila kuona wa ku Austria, amene amatsogoza Phunzilo la Nsanja ya Mlonda na Phunzilo la Baibo la Mpingo. Iye anati: “Mabuku athu ni osavuta kumva poyelekezela na mabuku ena amene naŵelengapo. Mwacitsanzo, mabuku athu amakhala na manambala a masamba, mawu a m’munsi osavuta kupeza, komanso mawu ofotokozela zithunzi omveka bwino.”

 Mlongo Seon-ok, ni mpainiya ku South Korea, amene ni wakhungu komanso wogontha. Kale, iye anali kudalila kumugwila manja na kumukambitsa m’cinenelo ca manja pa misonkhano. Koma tsopano amakwanitsa payekha kuŵelenga zofalitsa zophunzilila Baibo za anthu akhungu. Iye anati: “Mabuku ena a anthu akhungu ni ovuta kuwaŵelenga cifukwa mulibe zidindo zina, mizele ni yokhota-khota, kapena cifukwa anapangidwa na pepala lopepuka kwambili. Koma Mboni za Yehova zimaseŵenzetsa mapepala abwino, ndipo zidindo zake zimakhala zikulu-zikulu bwino cakuti cimakhala cosavuta kwa ine kuŵelenga.” Mlongoyo anakambanso kuti: “Kumbuyoku, n’nali kuŵelenga zofalitsa zophunzilila Baibo na thandizo la anthu ena. Koma tsopano nimadziŵelengela nekha. Nimakondwela kwambili kukonzekela misonkhano yacikhristu mlungu uliwonse na kutengako mbali mokwanila. Nimaŵelenga zofalitsa zathu zonse za akhungu. Ndipo nikayamba kuŵelenga, sinifuna kulekeza.”

 Mofanana na zofalitsa zopulintidwa za anthu amene amaona, zofalitsa zathu za anthu akhungu zili na mawu awa: “Cofalitsa cino si cogulitsa. Colinga cake ni kuthandiza pa nchito yophunzitsa Baibo imene ikucitika padziko lonse lapansi.” Nchito imeneyi timaiyendetsa na zopeleka zaufulu. Tikuyamikilani kaamba ka zopeleka zanu zimene mumapeleka mwa kuseŵenzetsa njila zofotokozedwa pa donate.dan124.com. Kuwoloŵa manja kwanu kumathandizila kuti anthu onse apeze cakudya cauzimu, kuphatikizapo akhungu komanso amene amavutikila kuona.

a Ena polemba mawu a anthu akhungu, amafupikitsako mawu kuti asawononge malo ambili. Mwacitsanzo, m’kalembedwe ka giledi 2 ka anthu akhungu, mawu odziŵika bwino komanso mawu ena amangowalemba mwacidule. Conco, buku la giledi 2 la anthu akhungu n’naling’ono poyelekezela na buku la giledi 1 la anthu akhungu.