Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 14

Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Lizisangalala

Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Lizisangalala
  • Kodi mwamuna wabwino ayenera kuchita chiyani?

  • Kodi mkazi angakwaniritse bwanji udindo wake m’banja?

  • Kodi munthu angatani kuti akhale kholo labwino?

  • Kodi ana angathandize bwanji kuti banja lonse lizisangalala?

1. Kodi n’chiyani chingathandize kuti banja likhale losangalala?

YEHOVA MULUNGU amafuna kuti mukhale ndi banja losangalala. Kudzera m’Mawu ake, Baibulo, iye amapereka malangizo kwa aliyense m’banja ndipo amafotokoza zimene aliyense ayenera kuchita. Onse m’banja akamakwaniritsa udindo wawo mogwirizana ndi malangizo a Mulungu, zinthu zimayenda bwino. Yesu anati: “Odala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!”—Luka 11:28.

2. Kodi timafunikira kuzindikira chiyani kuti tikhale ndi banja losangalala?

2 Kuti banja likhale losangalala, pamafunika kuzindikira kuti amene analiyambitsa ndi Yehova, yemwe Yesu anamutchula kuti “Atate wathu.” (Mateyu 6:9) Banja lililonse padziko lapansi pano linakhalapo chifukwa cha Atate wathu wakumwamba, choncho iye amadziwa bwino zimene zingapangitse kuti mabanja azikhala mosangalala. (Aefeso 3:14, 15) Ndiyeno, kodi Mawu a Mulungu amanena kuti aliyense ayenera kuchita chiyani m’banja?

MULUNGU NDI AMENE ANAYAMBITSA BANJA

3. Kodi Baibulo limafotokoza chiyani za chiyambi cha banja, ndipo tikudziwa bwanji kuti zimenezi ndi zoona?

3 Yehova analenga anthu oyambirira, Adamu ndi Hava ndipo anawakwatitsa kukhala banja. Iye anawaika padziko lapansi, m’munda wa Edeni n’kuwauza kuti abereke ana. Yehova anati: “Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anire.” (Genesis 1:26-28; 2:18, 21-24) Nkhaniyi si nthano chabe chifukwa Yesu anasonyeza kuti zimene zinalembedwa m’buku la Genesis zokhudza chiyambi cha banja n’zoona. (Mateyu 19:4, 5) Panopo tikukumana ndi mavuto ambiri ndipo moyo sulinso mmene Mulungu anafunira, komabe tiyeni tione zimene zingathandize kuti banja likhale losangalala.

4. (a) Kodi aliyense m’banja angathandize bwanji kuti banja likhale losangalala? (b) Kodi kuphunzira za Yesu n’kofunika bwanji kuti banja likhale losangalala?

4 Aliyense m’banja akamatsanzira Mulungu posonyeza chikondi, angathandize kuti banja likhale losangalala. (Aefeso 5:1, 2) Koma kodi tingatsanzire bwanji Mulungu amene sitingathe kumuona? Tingadziwe mmene Yehova amachitira zinthu chifukwa anatumiza Mwana wake padziko lapansi. (Yohane 1:14, 18) Pamene anali padziko lapansi, Yesu Khristu ankatsanzira kwambiri Atate wake wakumwamba moti kuona ndi kumvetsera zimene Yesu ankalankhula kunali ngati kukhala ndi Yehova n’kumamvetsera akulankhula. (Yohane 14:9) Choncho, kuphunzira za chikondi chimene Yesu anasonyeza ndi kutsatira chitsanzo chake kungathandize kuti tikhale ndi banja losangalala.

CHITSANZO CHABWINO KWA AMUNA OKWATIRA

5, 6. (a) Kodi mmene Yesu amachitira posamalira mpingo zikupereka bwanji chitsanzo kwa amuna okwatira? (b) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Mulungu azitikhululukira machimo athu?

5 Baibulo limapereka malangizo osonyeza kuti amuna ayenera kusamalira akazi awo ngati mmene Yesu ankachitira ndi ophunzira ake. Mwachitsanzo limati: “Amuna inu, pitirizani kukonda akazi anu monga mmene Khristu anakondera mpingo n’kudzipereka yekha chifukwa cha mpingowo . . . Mwa njira imeneyi amuna akonde akazi awo monga matupi awo. Amene amakonda mkazi wake amadzikonda yekha, pakuti palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda, mmenenso Khristu amachitira ndi mpingo.”Aefeso 5:23, 25-29.

6 Mmene Yesu ankakondera ophunzira ake ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa amuna okwatira. Yesu “anawakonda mpaka pa mapeto” ndipo anapereka moyo wake chifukwa cha ophunzirawo ngakhale kuti anali opanda ungwiro. (Yohane 13:1; 15:13) Choncho, amuna akulimbikitsidwa kuti: “Musaleke kukonda akazi anu ndipo musamawapsere mtima kwambiri.” (Akolose 3:19) Kodi n’chiyani chingathandize mwamuna kutsatira malangizo amenewa makamaka ngati mkazi wake nthawi zina amachita zinthu mosaganizira bwino? Mwamunayo ayenera kukumbukira kuti nayenso nthawi zina amalakwitsa zinthu ndipo amafunika kuchita zinazake kuti Mulungu amukhululukire. Kodi amafunika kuchita chiyani? Amafunika kukhululukira amene amulakwira ndipo anthu amenewo akuphatikizapo mkazi wake. Ndipo mkazi wake nayenso ayenera kuchita chimodzimodzi. (Werengani Mateyu 6:12, 14, 15.) Kodi mwaona chifukwa chake anthu ambiri amanena kuti banja ndi mgwirizano wa anthu awiri amene amakonda kukhululukirana?

7. Kodi Yesu nthawi zonse ankakumbukira chiyani za ophunzira ake, ndipo zimenezi zikupereka chitsanzo chotani kwa amuna okwatira?

7 Amuna okwatira ayeneranso kudziwa kuti Yesu nthawi zonse ankaganizira ophunzira ake. Iye ankawadziwa bwino mmene alili komanso zimene sakanakwanitsa kuchita. Mwachitsanzo, nthawi ina ophunzirawo atatopa iye anawauza kuti: “Bwerani kuno, tipite kwatokha kopanda anthu kuti mupumule pang’ono.” (Maliko 6:30-32) Akazinso amafunikira kuwaganizira mwachikondi. Baibulo limafotokoza kuti akazi ali ngati “chiwiya chosalimba” ndipo amuna akulamulidwa kuwapatsa “ulemu.” Chifukwa chiyani ayenera kuwapatsa ulemu? Chifukwa nawonso adzalandira moyo ‘umene Mulungu adzapereke chifukwa cha kukoma mtima kwake kwakukulu.’ (1 Petulo 3:7) Amuna ayenera kukumbukira kuti ndi kukhulupirika, osati kukhala mwamuna kapena mkazi, komwe kumachititsa munthu kukhala wamtengo wapatali kwa Mulungu.—Salimo 101:6.

8. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti “amene amakonda mkazi wake amadzikonda yekha”? (b) Kodi anthu amene ali pa banja angasonyeze bwanji kuti ndi “thupi limodzi”?

8 Baibulo limanena kuti mwamuna amene “amakonda mkazi wake amadzikonda yekha.” Izi zili choncho chifukwa Yesu ananena kuti mwamuna ndi mkazi akakwatirana sakhalanso awiri koma “thupi limodzi.” (Mateyu 19:6) Choncho, iwo ayenera kugonana ndi mwamuna kapena mkazi wawo yekha osati wina aliyense. (Miyambo 5:15-21; Aheberi 13:4) Angachite zimenezi ngati amaganizira zosowa za mnzawo osati zawo zokha. (1 Akorinto 7:3-5) Amuna azikumbukira malangizo ofunika akuti: “Palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda.” Amuna ayenera kukonda akazi awo mmene amadzikondera okha pokumbukira kuti adzafunsidwa ndi Yesu Khristu amene ndi mutu wawo.—Aefeso 5:29; 1 Akorinto 11:3.

9. Kodi pa Afilipi 1:8 patchulidwa khalidwe liti la Yesu, nanga n’chifukwa chiyani amuna ayenera kusonyeza khalidwe limeneli kwa akazi awo?

9 Mtumwi Paulo ananenapo za “chikondi chachikulu ngati chimene Khristu Yesu ali nacho.” (Afilipi 1:8) Anthu ankalimbikitsidwa poona mmene Yesu ankawakondera, makamaka akazi amene anakhala ophunzira ake. (Yohane 20:1, 11-13, 16) Akazi okwatiwa amafunanso kuti amuna awo aziwakonda.

CHITSANZO CHABWINO KWA AKAZI OKWATIWA

10. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani kwa akazi okwatiwa?

10 Banja lili ngati kampani. Kuti liziyenda bwino pamafunikira mutu. Ngakhalenso Yesu ali ndi Mutu umene amaugonjera. ‘Mutu wa Khristu ndi Mulungu’ monganso mmene zilili kuti “mutu wa mkazi ndi mwamuna.” (1 Akorinto 11:3) Zimene Yesu amachita pogonjera Mulungu monga Mutu wake, n’chitsanzo chabwino kwambiri chifukwa tonsefe tili ndi wina amene tiyenera kumugonjera.

11. Kodi mkazi ayenera kusonyeza khalidwe lotani kwa mwamuna wake, ndipo ubwino wake ndi wotani?

11 Popeza kuti nawonso amuna ndi opanda ungwiro, nthawi zina amalakwitsa zinthu ndipo amalephera kukhala mitu yabwino ya mabanja awo. Ndiye zikakhala choncho, kodi mkazi azichita chiyani? Iye sayenera kunyoza zimene mwamuna wake akuchita kapena kulanda udindo wa mwamuna wake. Mkazi ayenera kukumbukira kuti Mulungu amaona kuti akazi amene ali ndi mzimu wofatsa ndi amtengo wapatali. (1 Petulo 3:4) Akazi akamasonyeza khalidwe limeneli, savutika kukhala ogonjera ngakhale pamene zinthu sizili bwino. Ndipotu Baibulo limanena kuti: “Mkazi azilemekeza kwambiri mwamuna wake.” (Aefeso 5:33) Nanga bwanji ngati mwamunayo saona Khristu ngati Mutu wake? Baibulo limalimbikitsabe akazi kuti: “Muzigonjera amuna anu kuti ngati ali osamvera mawu akopeke, osati ndi mawu, koma ndi khalidwe lanu, poona okha ndi maso awo khalidwe lanu loyera ndi ulemu wanu waukulu.”1 Petulo 3:1, 2.

12. N’chifukwa chiyani si kulakwa ngati mkazi atafotokoza maganizo ake mwaulemu?

12 Kaya mwamuna wake ndi wokhulupirira kapena ayi, si kuti mkazi akafotokoza maganizo osiyana ndi amwamuna wakeyo pa nkhani inayake ndiye kuti alibe ulemu. Maganizo akewo akhoza kukhala olondola ndipo mwina banja lonse lingapindule ngati litatsatira zimene akunenazo. Mwachitsanzo, nthawi ina Abulahamu sanagwirizane ndi maganizo a mkazi wake, Sara, okhudza njira inayake yothetsera vuto lomwe linali m’banja lawo. Koma Mulungu anamuuza kuti: “Mvera mawu ake.” (Werengani Genesis 21:9-12.) Komabe ngati zimene mwamuna wake wasankha sizikusemphana ndi malamulo a Mulungu, mkazi ayenera kugonjera.—Machitidwe 5:29; Aefeso 5:24.

Kodi Sara anapereka chitsanzo chotani kwa akazi okwatiwa?

13. (a) Kodi lemba la Tito 2:4, 5 limalimbikitsa akazi okwatiwa kuchita chiyani? (b) Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani ya kusiyana ndiponso kuthetsa banja?

13 Pali zambiri zimene mkazi angachite kuti akwaniritse udindo wake wosamalira banja. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti akazi okwatiwa ayenera “kukonda amuna awo, kukonda ana awo, kukhala oganiza bwino, oyera, ogwira ntchito zapakhomo, abwino ndi ogonjera amuna awo.” (Tito 2:4, 5) Mkazi amene amasonyeza makhalidwe amenewa kwa mwamuna wake komanso ana ake, amakondedwa komanso kulemekezedwa ndi banja lake. (Werengani Miyambo 31:10, 28.) Popeza kuti banja ndi mgwirizano wa anthu awiri opanda ungwiro, nthawi zina pangakhale mavuto akuluakulu amene angapangitse kuti mwamuna ndi mkazi asiyane kwa kanthawi kapena kuti banja lithe. Baibulo limalola kuti mwamuna ndi mkazi asiyane pakakhala mavuto ena. Komabe ngakhale zili choncho, imeneyi si nkhani yaing’ono chifukwa Baibulo limanena kuti: “Mkazi asasiye mwamuna wake, . . . mwamunanso asasiye mkazi wake.” (1 Akorinto 7:10, 11) Malemba amalola kuti banja lingathe pokhapokha ngati mwamuna kapena mkazi wachita chigololo.—Mateyu 19:9.

CHITSANZO CHABWINO KWA MAKOLO

14. Kodi Yesu ankachita bwanji zinthu ndi ana, nanga ana amafuna makolo awo azichita chiyani?

14 Mmene Yesu ankachitira zinthu ndi ana ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa makolo. Pamene ena ankafuna kuletsa ana kuti asayandikire Yesu, iye anati: “Alekeni anawo abwere kwa ine, musawaletse ayi.” Baibulo limanena kuti kenako iye “anatenga anawo m’manja mwake ndi kuyamba kuwadalitsa.” (Maliko 10:13-16) Popeza kuti Yesu anapeza nthawi yocheza ndi ana, kodi inunso simungachite chimodzimodzi ndi ana anu? Ana amafunika nthawi yambiri yocheza nawo. Muyenera kukhala ndi nthawi yokwanira yowaphunzitsa chifukwa zimenezi ndi zomwe Yehova amafuna kuti makolo azichita.—Werengani Deuteronomo 6:4-9.

15. Kodi makolo angatani kuti ateteze ana awo?

15 Pamene dzikoli likuipiraipirabe, makolo amafunika kuteteza ana awo kwa ogwiririra ana komanso kwa anthu ena amene angafune kuwavulaza. Taganizirani mmene Yesu anatetezera ophunzira ake, omwe anawatchula mwachikondi kuti “ana apamtima.” Adani ake atamugwira kuti akamuphe, iye anayesetsa kuteteza ophunzira akewo kuti asagwidwe. (Yohane 13:33; 18:7-9) Monga makolo, muyenera kuonetsetsa kuti ana anu ndi otetezeka kwa Mdyerekezi amene amafuna kuwavulaza. Muyeneranso kuwachenjezeratu pasadakhale. * (1 Petulo 5:8) Panopa moyo wauzimu wa ana komanso makhalidwe awo zili pa ngozi yaikulu kuposa kale.

Kodi makolo angaphunzire chiyani kwa Yesu poona mmene ankachitira zinthu ndi ana?

16. Kodi makolo angaphunzire chiyani kwa Yesu poona zimene ankachita ophunzira ake akalakwitsa zinthu zina?

16 Usiku woti Yesu aphedwa mawa, ophunzira ake anakangana pa nkhani yakuti wamkulu ndani pakati pawo. M’malo mowakalipira, Yesu anapitiriza kuwalangiza mokoma mtima ndi kuwapatsa chitsanzo. (Luka 22:24-27; Yohane 13:3-8) Ngati muli ndi ana, kodi mwaona mmene mungatsanzirire chitsanzo cha Yesu polangiza ana anu? N’zoona kuti ana amafunikira chilango koma chiyenera kuperekedwa “pa mlingo woyenera,” osati mwaukali. Simuyenera kugwiritsa ntchito mawu olakwika, omwe amakhala “olasa ngati lupanga.” (Yeremiya 30:11; Miyambo 12:18) Chilango chiyenera kuperekedwa moyenera kuti mwanayo pambuyo pake azitha kuona kuti chinalidi chofunika.—Aefeso 6:4; Aheberi 12:9-11.

CHITSANZO CHABWINO KWA ANA

17. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani kwa ana?

17 Kodi pali zimene ana angaphunzire kuchokera kwa Yesu? Inde zilipo. Zimene Yesu ankachita zingathandize ana kuti azimvera makolo awo. Iye anati: “Ndimalankhula zinthu . . . ndendende mmene Atate anandiphunzitsira.” Ndipo anawonjezeranso kuti: “Ndimachita zinthu zomukondweretsa nthawi zonse.” (Yohane 8:28, 29) Yesu ankamvera Atate wake wakumwamba, ndipo Baibulo limauza achinyamata kuti nawonso azimvera makolo awo. (Werengani Aefeso 6:1-3.) Ngakhale kuti Yesu anali wangwiro, ali mwana ankamverabe makolo ake, Yosefe ndi Mariya, omwe anali opanda ungwiro. Zimenezi ziyenera kuti zinathandiza kuti anthu onse m’banja mwawo azikhala mosangalala.—Luka 2:4, 5, 51, 52.

18. N’chifukwa chiyani nthawi zonse Yesu ankamvera Atate ake, nanga masiku ano ndi ndani amene amasangalala ana akamamvera makolo awo?

18 Kodi ana angatsanzire bwanji chitsanzo cha Yesu, zomwe zingachititse kuti makolo awo azisangalala? Nthawi zina ana angaone kuti kumvera makolo awo n’kovuta, komabe zimenezi ndi zomwe Mulungu amafuna kuti azichita. (Miyambo 1:8; 6:20) Kumbukirani kuti Yesu ankamvera Atate wake wakumwamba ngakhale pamene kuchita zimenezo kunali kovuta. Nthawi ina, pamene Mulungu anamuuza kuti achite zinthu zina zovuta, Yesu ananena kuti: “Ndichotsereni kapu iyi.” Ngakhale ananena mawu amenewa, iye anachitabe zimene Mulungu ankafuna, chifukwa ankadziwa kuti Atate wake akudziwa zonse. (Luka 22:42) Ana akakhala omvera, amasangalatsa makolo awo komanso Atate wawo wakumwamba. *Miyambo 23:22-25.

Kodi achinyamata ayenera kukumbukira chiyani akakumana ndi mayesero?

19. (a) Kodi Satana amawayesa bwanji ana? (b) Kodi khalidwe loipa la ana lingakhudze bwanji makolo awo?

19 Ngati Mdyerekezi anayesa Yesu, sitingakayikire zoti adzayesanso ana anu kuti achite zinthu zoipa. (Mateyu 4:1-10) Nthawi zina Satana Mdyerekezi angachititse anzawo a anawo kuti awanyengerere kuchita zinthu zoipa ndipo zimenezi zimakhala zovuta kwambiri kuzipewa. Choncho ndi bwino kuti ana azipewa kucheza ndi anthu oipa. (1 Akorinto 15:33) Dina, mwana wa Yakobo, ankakonda kucheza ndi anthu amene sankatumikira Yehova ndipo zimenezi zinachititsa kuti akumane ndi mavuto. (Genesis 34:1, 2) Taganizirani mmene banja lonse lingamvere ngati wina m’banjamo atachita chiwerewere.—Miyambo 17:21, 25.

CHINSINSI CHA BANJA LOSANGALALA

20. Kuti banja likhale losangalala, kodi aliyense m’banjamo ayenera kuchita chiyani?

20 Mavuto a m’banja savuta kuwapirira ngati anthu a m’banjamo akutsatira malangizo a m’Baibulo. Ndipotu kutsatira malangizo amenewa ndi chinsinsi chokhalira ndi banja losangalala. Choncho amuna muyenera kukonda akazi anu ngati mmene Yesu amachitira ndi mpingo wake. Akazi muyenera kugonjera amuna anu ndiponso kutsatira chitsanzo chabwino cha mkazi wotchulidwa pa Miyambo 31:10-31. Makolo muyenera kuphunzitsa ana anu. (Miyambo 22:6) Abambo, ‘muziyang’anira bwino banja lanu.’ (1 Timoteyo 3:4, 5; 5:8) Ndipo ana muyenera kumvera makolo anu. (Akolose 3:20) Popeza tonse ndife ochimwa, palibe amene angachite zinthu zolondola zokhazokha. Choncho muyenera kukhala odzichepetsa n’kumapepesa pamene mwalakwitsa.

21. Kodi tikuyembekezera chiyani m’tsogolo, nanga panopa tingachite chiyani kuti banja lathu likhale losangalala?

21 Kunena zoona, Baibulo lili ndi malangizo ofunika kwambiri othandiza kuti mabanja aziyenda bwino. Limatiphunzitsanso za dziko latsopano la paradaiso momwe mudzakhale anthu osangalala amene amalambira Yehova. (Chivumbulutso 21:3, 4) Kutsogoloku kulidi zinthu zosangalatsa kwambiri. Koma ngakhale panopa, tikhoza kukhala ndi banja losangalala tikamatsatira malangizo a Mulungu opezeka m’Mawu ake, Baibulo.

^ ndime 15 Mungapeze mfundo zokuthandizani kuteteza ana anu m’Mutu 32 m’buku lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 18 Pokhapokha ngati makolo akufuna kuti mwana aphwanye malamulo a Mulungu m’pamene zingakhale zoyenera kuti mwanayo asawamvere.—Machitidwe 5:29.