Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Makhalidwe abwino ali ngati kampasi yomwe ingathandize mwana wanu kudziwa zoyenera kuchita

MAKOLO

7: Makhalidwe

7: Makhalidwe

ZIMENE ZIMACHITIKA

Mawu akuti “makhalidwe” amafotokoza za mfundo zomwe mumakhazikitsa kuti muziyendera. Mwachitsanzo, ngati mumayesetsa kukhala wokhulupirika pa zonse zomwe mumachita, n’zodziwikiratu kuti mungakonde kuti ana anu azichitanso zomwezo.

Munthu wakhalidwe amayenderanso mfundo zoyenera. Mwachitsanzo, amakhala wakhama, wachilungamo komanso amachita zinthu moganizira ena. Ndipo ana amafunika kuphunzitsidwa makhalidwewa adakali aang’ono.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Phunzitsa mwana m’njira yomuyenerera. Ngakhale akadzakalamba sadzapatukamo.”​—Miyambo 22:6.

N’CHIFUKWA CHIYANI KUGANIZIRA NKHANIYI N’KOFUNIKA?

Kukhala wakhalidwe ndi kofunika kwambiri makamaka panopo. Mayi wina dzina lake Karyn ananena kuti: “Masiku ano anthu akhoza kupeza zinthu zoipa pa zipangizo zamakono nthawi iliyonse. Tikhoza kukhala limodzi ndi ana athu kwinaku akuoneranso zinthu zoipa.”

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Anthu okhwima mwauzimu, [ndi] amene pogwiritsa ntchito mphamvu zawo za kuzindikira, aphunzitsa mphamvuzo kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.”​—Aheberi 5:14.

Kutsatira mfundo zoyenera n’kofunika kwambiri. Zimenezi zingaphatikizepo kupempha zinthu mwaulemu, kuthokoza komanso kuchita zinthu moganizira ena. Masiku ano anthu ambiri amangochita chidwi ndi zipangizo zawo zamakono osati ndi anzawo.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muwachitire zomwezo.”​—Luka 6:31.

ZIMENE MUNGACHITE

Muziwauza mfundo za makhalidwe abwino. Mwachitsanzo, ochita kafukufuku anapeza kuti achinyamata amapewa kugonana asanalowe m’banja akauzidwa momveka bwino za kuopsa kwa khalidweli.

TAYESANI IZI: Mukafuna kukambirana ndi ana anu zokhudza makhalidwe abwino, yambani ndi kufotokoza zomwe zangochitika kumene. Mwachitsanzo, ngati mwamvetsera nkhani zonena kuti kwachitika za chiwawa, munganene kuti: “N’zovuta kumvetsa kuti anthu ena amachitira anzawo zinthu zankhanza chonchi. Ukuganiza kuti anthuwa akuchitiranji zimenezi?”

A Brandon ananena kuti: “N’zovuta kwambiri kuti ana azitha kusiyanitsa chabwino ndi choipa ngati sakudziwa kuti zabwino ndi zoipazo ndi ziti.”

Muziwaphunzitsa mfundo zoyenera. Ana aang’ono nawonso akhoza kuphunzira kupempha zinthu mwaulemu, kuthokoza komanso kuchita zinthu moganizira ena. Buku lina linanena kuti: “Ana akadziwa kuti nawonso ndi ofunika m’banja, kusukulu kapena m’deralo, amachita zinthu mokoma mtima ndipo sakhala ndi mtima wodzikonda.”​—Parenting Without Borders.

TAYESANI IZI: Muzipatsa ana anu ntchito za pakhomo kuti azidziwa kufunika kothandiza ena.

A Tara ananena kuti: “Ana akamapatsidwa ntchito za pakhomo sangadzavutike akadzakhala paokha chifukwa amakhala atazolowera kale.”