Pitani ku nkhani yake

Kodi Kubweranso kwa Yesu Kumatanthauza Chiyani?

Kodi Kubweranso kwa Yesu Kumatanthauza Chiyani?

Yankho la m’Baibulo

 M’Baibulo muli malemba ambiri osonyeza kuti Yesu adzabwera kudzaweruza anthu onse. a Mwachitsanzo, lemba la Mateyu 25:31-33 limanena kuti:

 “Mwana wa munthu akadzafika mu ulemerero wake, limodzi ndi angelo ake onse, adzakhala pampando wake wachifumu waulemerero. Mitundu yonse ya anthu idzasonkhanitsidwa kwa iye ndipo adzalekanitsa anthu, mmene m’busa amalekanitsira nkhosa ndi mbuzi. Adzaika nkhosa kudzanja lake lamanja, koma mbuzi adzaziika kumanzere kwake.”

 Tsiku la chiweruzo limeneli, lidzakhala mbali ya “chisautso chachikulu,” chomwe sichinachitikepo m’mbiri yonse ya anthu. Chisautso chimenechi chidzafika pampondachimera pa nkhondo ya Aramagedo. (Mateyu 24:21; Chivumbulutso 16:16) Adani Akhristu omwe m’fanizo lija atchulidwa kuti mbuzi, “adzawaweruza kuti alandire chilango cha chiwonongeko chamuyaya.” (2 Atesalonika 1:9; Chivumbulutso 19:11, 15) Koma anthu okhulupirika, omwe ali ngati nkhosa, adzalandira “moyo wosatha.”​—Mateyu 25:46.

Kodi Khristu adzabwera Liti?

 Yesu ananena kuti: “Kunena za tsikulo ndi ola lake, palibe amene akudziwa.” (Mateyu 24:36, 42; 25:13) Komabe Yesu anatchula zizindikiro zomwe zikanathandiza anthu kudziwa kuti akukhala m’masiku otsiriza.​—Mateyu 24:3, 7-14; Luka 21:10, 11.

Kodi Yesu akadzabwera, anthu adzamuona?

 Yesu anaukitsidwa ndi thupi la uzimu. Choncho anali ndi thupi ngati la angelo, osati ngati la munthu. (1 Akorinto 15:45; 1 Petulo 3:18) N’chifukwa chake kutatsala tsiku limodzi kuti aphedwe, Yesu anauza atumwi ake kuti: “Kwatsala kanthawi pang’ono ndipo dziko silidzandionanso.”—Yohane 14:19.

Maganizo olakwika amene anthu amakhala nawo ponena za kubwera kwa Yesu

 Maganizo olakwika: Baibulo likamanena kuti Yesu “akubwera pamitambo ya kumwamba,” limatanthauza kuti aliyense adzamuona akubwera.​—Mateyu 24:30.

 Zoona zake: Nthawi zambiri Baibulo likamanena za mitambo, limanena za chinthu chimene anthu sangachione. (Levitiko 16:2; Numeri 11:25; Deuteronomo 33:26) Mwachitsanzo, Mulungu anauza Mose kuti: “Nditsikira kwa iwe mumtambo wakuda.” (Ekisodo 19:9) Sikuti Mose anamuonadi Mulungu. Mofanana ndi zimenezi, nayenso Yesu adzabwera m’mitambo. Zimenezi zikutanthauza kuti anthu sadzamuona, koma adzazindikira kuti wabwera.

 Maganizo olakwika: Mawu omwe ali pa Chivumbulutso 1:7 akuti “diso lililonse lidzamuona,” tiyenera kungowatenga mmene alili.

 Zoona zake: Mawu Achigiriki omwe anawamasulira m’Baibulo kuti “diso” ndiponso “lidzamuona,” nthawi zina angatanthauze kuzindikira, osati kuona chinachake ndi maso athu. b (Mateyu 13:15; Luka 19:42; Aroma 15:21; Aefeso 1:18) Baibulo limanena kuti, Yesu ataukitsidwa anapita kumalo kumene “palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene . . . angamuone.” (1 Timoteyo 6:16) Choncho mawu akuti “diso lililonse lidzamuona,” akutanthauza kuti anthu adzazindikira kuti Yesu wabwera kudzaweruza anthu.​—Mateyu 24:30.

 Maganizo olakwika: Mawu amene ali pa lemba la 2 Yohane 7, akusonyeza kuti Yesu adzabwera ngati munthu.

 Zoona zake: Lembali limanena kuti: “Anthu onyenga ambiri alowa m’dziko, amene amatsutsa zakuti kalero Yesu Khristu anabwera monga munthu.”

 M’nthawi yomwe mtumwi Yohane ankalemba mawuwa, anthu ambiri ankakana zoti Yesu anabwera padzikoli monga munthu. Choncho mtumwiyo analemba kalatayi pofuna kutsutsa zimenezi.

a Ngakhale kuti anthu ambiri amagwiritsa ntchito mawu akuti “kubweranso kwachiwiri” kwa Ambuye ponena za kubwera kwa Yesu, mawu amenewa sapezeka m’Baibulo.

b Onani buku lakuti, The New Thayer’s Greek-English Lexicon of the New Testament (1981), tsamba 451 ndi 470.