Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 13

Mmene Zipembedzo Zonyenga Zimaimilako Mulungu Monama

Mmene Zipembedzo Zonyenga Zimaimilako Mulungu Monama

Mulungu ndiye cikondi. Koma n’cifukwa ciyani zipembedzo zimacita zoipa zambili m’dzina la Mulungu? Kunena mosapita m’mbali, zipembedzo zimenezo ni zonyenga, zimaimilako Mulungu monama. Kodi zimamuimilako monama m’njila ziti? Nanga Mulungu amamvela bwanji poona zimenezo? Ndipo adzacitapo ciyani?

1. Zipembedzo zonyenga zimaimilako Mulungu monama mwa ziphunzitso zawo—motani?

Zipembedzo zonyenga ‘zasinthanitsa coonadi ca Mulungu ndi bodza.’ (Aroma 1:25) Mwacitsanzo, zipembedzo zoculuka siziphunzitsa anthu awo dzina la Mulungu. Koma Baibo imanena kuti tiyenela kumalichula dzina la Mulungu. (Aroma 10:13, 14) Ndipo atsogoleli ena a zipembedzo, cinthu coipa cikacitika amakamba kuti ni cifunilo ca Mulungu. Koma limenelo ni bodza lamkunkhuniza. N’zosatheka kuti Mulungu acititse coipa ciliconse. (Ŵelengani Yobu 34:12.) Cifukwa ca mabodza a zipembedzo amenewo, cakhala covuta kwa anthu ena kuti amukonde Mulungu. Zimenezi n’zacisoni kwambili.

2. Zipembedzo zonyenga zimaimilako Mulungu monama mwa zocita zawo—motani?

Zipembedzo zonyenga sizisamala za anthu mmene Yehova amacitila. Kunena za zipembedzo zonyenga, Baibo imakamba kuti, “macimo ake aunjikana mpaka kumwamba.” (Chivumbulutso 18:5) Kwa zaka mahandiledi, zipembedzo zaloŵelela m’nkhani zandale, zalimbikitsa nkhondo, ndipo zacititsa imfa za anthu ambili-mbili. Atsogoleli ena a zipembedzo amalemela kwambili cifukwa ca ndalama zimene amakakamiza anthu awo kumapeleka. Zocitika zimenezi zimatsimikizila kuti Mulungu samudziŵa n’komwe, conco ni osayenelela kumuimilako.—Ŵelengani 1 Yohane 4:8.

3. Kodi Mulungu amaziona bwanji zipembedzo zonyenga?

Ngati inu mumakwiya poona zocita za zipembedzo zonyenga, nanga Yehova muganiza amamvela bwanji? Mulungu amakonda anthu. Koma amakwiya na atsogoleli a zipembedzo amene amamuimilako monama, amenenso amadyela masuku pamutu anthu awo. Iye akulonjeza kuti zipembedzo zonyenga zidzawonongedwa, ndipo sizidzapezekanso. (Chivumbulutso 18:21) Posacedwa Mulungu adzawononga zipembedzo zonse zonyenga.—Chivumbulutso 18:8.

KUMBANI MOZAMILAPO

Dziŵani zambili zokhudza mmene Mulungu amaonela zipembedzo zonyenga. Onani zinanso zimene zipembedzo zacita, komanso cifukwa cake siziyenela kukulepheletsani kumudziŵa Yehova.

4. Mulungu savomeleza zipembedzo zonse

Anthu ambili amakhulupilila kuti zipembedzo zili monga njila zosiyana-siyana zopita kwa Mulungu. Kodi zimenezi n’zoona? Ŵelengani Mateyu 7:13, 14, na kukambilana funso ili:

  • Kodi Baibo imati ciyani ponena za njila ya ku moyo?

Tambani VIDIYO, na kukambilana funso ili.

  • Kodi Baibo imakamba kuti zipembedzo zambili n’zovomelezeka kwa Mulungu?

5. Zipembedzo zonyenga sizionetsa cikondi ca Mulungu

Zipembedzo zaimilako Mulungu monama m’njila zambili. Njila imodzi yoipitsitsa kwambili ni kuloŵelela kwawo pa nkhondo. Kuti muone citsanzo cimodzi, tambani VIDIYO. Ndiyeno kambilanani mafunso aya.

  • Pa nkhondo yaciŵili yapadziko lonse, kodi machalichi ambili anacita ciyani?

  • Inu muona bwanji pa zimene anacitazo?

Ŵelengani Yohane 13:34, 35 komanso 17:16. Ndiyeno kambilanani mafunso aya:

  • Kodi Yehova amamva bwanji ngati zipembedzo ziloŵelela pa nkhondo?

  • Zipembedzo zacititsa zinthu zoipa zambili. Kodi inu muona kuti zipembedzo zalephela kuonetsa cikondi ca Mulungu m’njila zotani?

Zipembedzo zonyenga zalephela kuonetsa cikondi ca Mulungu

6. Mulungu amafuna kuthandiza anthu kuti acoke m’zipembedzo zonyenga

Ŵelengani Chivumbulutso 18:4, a na kukambilana funso ili:

  • Kodi mukumva bwanji podziŵa kuti Mulungu amafuna kupulumutsa anthu amene cipembedzo conyenga cawasoceletsa?

7. Pitilizani kuphunzila za Mulungu woona

Kodi zinthu zoipa zimene zipembedzo zonyenga zimakamba kapena kucita ziyenela kusintha mmene mumamuonela Mulungu? Tiyelekeze kuti mnyamata wakana malangizo a nzelu a atate ŵake, wacoka pakhomo, na kuyamba umoyo wocita zinthu zoipa. Atate ŵake sagwilizana na zimene mwana wawo wacita. Poona umoyo wopanduka umene mwanayo akukhala, n’cifukwa ciyani sicingakhale cilungamo kupatsa mlandu atate ŵake?

  • Kodi cingakhale canzelu kuimba mlandu Yehova, na kuleka kuphunzila za iye, cifukwa ca zimene zipembedzo zonyenga zimacita?

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Ine sinikonda kukambilana za cipembedzo, cifukwa zipembedzo ndiye zabweletsa mavuto ambili-mbili.”

  • Kodi ni mmene inunso mukuonela?

  • N’cifukwa ciyani zocita za zipembedzo zonyenga siziyenela kukhudza mmene timaonela Yehova?

CIDULE CAKE

Zipembedzo zonyenga zimaimilako Mulungu monama mwa ziphunzitso zawo zabodza komanso zocita zawo zoipa. Mulungu adzawononga zipembedzo zonse zonyenga.

Mafunso Obweleza

  • Mumamva bwanji mukaona zimene zipembedzo zonyenga zimaphunzitsa komanso zocita zawo?

  • Kodi Yehova amaziona bwanji zipembedzo zonyenga?

  • Nanga Mulungu adzacita nazo bwanji zipembedzo zonyenga?

Colinga

FUFUZANI

Dziŵani njila ziŵili zimene zipembedzo zambili zimakwiyitsa nazo Mulungu.

“Kodi Zipembedzo Zonse N’cimodzi-modzi? Kodi Zonse Zimatsogolela kwa Mulungu?” (Nkhani ya pawebusaiti)

N’cifukwa ciyani Yehova amafuna kuti tizimulambila pamodzi na anthu ŵena?

“Kodi N’kofunikila Kukhala na Cipembedzo?” (Nkhani ya pawebusaiti)

Wansembe wina anakhumudwa na cipembedzo cake. Ngakhale n’telo, iye sanaleke kuphunzila coonadi ponena za Mulungu.

“N’cifukwa Ciani Wansembe Anasiya Cipembedzo Cake?” (Galamuka!, February 2015)

Kwa zaka mazana ambili, zipembedzo zakhala zikuphunzitsa mabodza ponena za Mulungu. Izi zapangitsa anthu kuona kuti Mulungu sasamala za ife ndipo ni wankhanza. Dziŵani zoona zake pa mabodza atatu otelo.

“Mabodza Amene Amalepheletsa Anthu Kukonda Mulungu” (Nsanja ya Mlonda, November 1, 2013)

a Kuti mudziŵe cimene buku la Chivumbulutso limachulila cipembedzo conyenga kuti ni mkazi wochedwa Babulo Wamkulu, onani Mfundo Yakumapeto 1.