Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 27

Kodi Imfa ya Yesu Ingatipulumutse Bwanji?

Kodi Imfa ya Yesu Ingatipulumutse Bwanji?

Cifukwa cakuti anthu aŵili oyambilila, Adamu na Hava, sanamvele Mulungu, ife anthu timacimwa, timakumana na mavuto, ndiponso timamwalila. a Koma sikuti tilibiletu ciyembekezo. Yehova popeleka Mwana wake Yesu Khristu, anakonza njila yotipulumutsila ku tembelelo la ucimo na imfa. Baibo imatiphunzitsa kuti Yesu anapeleka dipo potifela. Dipo ni malipilo opelekedwa kuwombola munthu. Conco, malipilo amene Yesu anapeleka ni moyo wake wangwilo monga munthu padziko lapansi. (Ŵelengani Mateyu 20:28.) Popeza Yesu anabadwa monga munthu wangwilo, mwacibadwa anali na ufulu wokhala na moyo wosatha padziko lapansi. Koma pamene anadzipeleka mu imfa, iye anadzimana ufulu umenewo, kuti atitsegulile njila yokapezela zonse zimene Adamu na Hava anataya. Ndipo Yesu anaonetsanso kuti iye na Yehova amatikonda kwambili. Phunzilo lino likuthandizeni kuyamikila kwambili imfa ya Yesu.

1. Kodi imfa ya Yesu ingatipindulile bwanji masiku ano?

Pokhala anthu ocimwa, timacita zinthu zambili zokhumudwitsa Yehova. Komabe, ngati tikhaladi acisoni pa macimo amene tacita, na kulapa mocokela pansi pa mtima, kenako n’kupempha kwa Yehova kupitila mwa Yesu Khristu kuti atikhululukile, na kuyesetsa kuti tisakacitenso zimene tinalakwazo, tingakhale pa ubwenzi wolimba na Mulungu. (1 Yohane 2:1) Baibo imanena kuti: “Khristu anafela macimo kamodzi kokha basi. Munthu wolungamayo anafela anthu osalungama, kuti akufikitseni kwa Mulungu.”1 Petulo 3:18.

2. Kodi imfa ya Yesu idzatipindulila bwanji m’tsogolo?

Yehova anatuma Yesu Khristu kuti adzapeleke moyo wake wangwilo monga munthu, “kuti aliyense wokhulupilila [mwa Yesu] asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Cifukwa ca zimene Yesu anacita, posacedwa Yehova adzacotsapo zoipa zonse zimene kusamvela kwa Adamu kunabweletsa. Izi zitanthauza kuti tikakhala na cikhulupililo mu nsembe ya Yesu Khristu, tidzapeza moyo wamuyaya m’paradaiso padziko lapansi!—Yesaya 65:21-23.

KUMBANI MOZAMILAPO

Phunzilani zambili pa cifukwa cimene Yesu anapelekela moyo wake, komanso mmene mungapindulile.

3. Imfa ya Yesu imatimasula ku ucimo na imfa

Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.

  • Kodi Adamu anataya mwayi wanji pamene anapandukila Mulungu?

Ŵelengani Aroma 5:12, na kukambilana funso ili:

  • Kodi chimo la Adamu linakhudza bwanji umoyo wanu?

Ŵelengani Yohane 3:16, na kukambilana funso ili:

  • N’cifukwa ciyani Yehova anatumiza Mwana wake padziko lapansi?

  1. Adamu anali munthu wangwilo, koma anapandukila Mulungu na kuika anthu pa njila ya ucimo na imfa

  2. Yesu anali munthu wangwilo, ndipo anamvela Mulungu na kuika anthu pa njila yopita ku moyo wangwilo wamuyaya

4. Imfa ya Yesu ni yopindulila anthu onse

Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.

  • Kodi imfa ya munthu mmodzi ingapindulile bwanji anthu onse?

Ŵelengani 1 Timoteyo 2:5, 6, na kukambilana funso ili:

  • Adamu anali munthu wangwilo, koma anaika anthu pa njila ya ucimo na imfa. Yesu nayenso anali munthu wangwilo. Kodi Yesu anapeleka “dipo lokwanila ndendende” m’njila yotani?

5. Dipo ni mphatso ya Yehova kwa inu

Mabwenzi a Yehova amaona kuti dipo ni mphatso imene anapatsidwa aliyense payekha. Mwacitsanzo, ŵelengani Agalatiya 2:20, na kukambilana funso ili:

  • Kodi mtumwi Paulo anaonetsa bwanji kuti anali kuona dipo kukhala mphatso yopelekedwa kwa iye payekha?

Pamene Adamu anacimwa, iye komanso mbadwa zake zonse analandila tembelelo la imfa. Koma Yehova anatumiza Mwana wake kudzatifela kuti tikalandile moyo wosatha.

Pamene muŵelenga mavesi otsatilawa, tangoganizilani mmene Yehova zinam’khudzila poona Mwana wake akuzunzika. Ŵelengani Yohane 19:1-7, 16-18, na kukambilana funso ili:

  • Kodi mumamva bwanji mukaganizila zimene Yehova na Yesu anakucitilani?

MUNTHU WINA ANGAFUNSE KUTI: “Kodi zingatheke bwanji kuti imfa ya munthu mmodzi n’kupulumutsa anthu onse?”

  • Kodi mungayankhe bwanji?

CIDULE CAKE

Imfa ya Yesu ndiyo maziko amene Yehova amatikhululukilapo macimo athu, ndipo imatipatsa mwayi wokapeza moyo wamuyaya.

Mafunso Obweleza

  • N’cifukwa ciyani Yesu anafa?

  • Kodi moyo wangwilo wa Yesu unali dipo lokwanila ndendende m’njila yanji?

  • Kodi imfa ya Yesu ingakupindulileni motani?

Colinga

FUFUZANI

Dziŵani cifukwa cake moyo wangwilo wa Yesu monga munthu padziko lapansi umachedwa dipo.

“Kodi Nsembe ya Yesu Imawombola Bwanji ‘Anthu Ambiri’?” (Nkhani ya pawebusaiti)

Pezani zimene tiyenela kucita kuti tikapulumuke.

“Kodi Yesu Amatipulumutsa Bwanji?” (Nkhani ya pawebusaiti)

Kodi Yehova angakhululuke ngakhale macimo akulu-akulu?

“Kuyankha Mafunso a m’Baibo” (Nsanja ya Mlonda, May 1, 2013)

Onani mmene kuphunzila za nsembe ya Khristu kunathandizila munthu wina amene poyamba anali kuvutika mumtima akakumbukila zinthu zakale zosautsa maganizo.

“Si Inenso Kapolo wa Chiwawa” (Nkhani ya pawebusaiti)

a Kucimwa sikutanthauza cabe kucita cinthu coipa ayi. Kumatanthauzanso cibadwa caucimo cimene tinatengela kwa Adamu na Hava.