Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Dzina la Mulungu linalembedwa mu mipukutu yakale ya Baibulo

Kodi Baibulo Limakamba Ciani?

Kodi Baibulo Limakamba Ciani?

Kodi Mulungu ali ndi dzina?

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI alibe dzina, ena amati dzina lake ndi Mulungu kapena Ambuye, ndipo ena amati ali ndi maina ambili. Nanga inu muganiza bwanji?

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA

“Dzina lanu ndinu Yehova, Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulila dziko lonse lapansi.”—Salimo 83:18.

ZINA ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA

  • Ngakhale kuti Mulungu ali ndi maina ambili audindo, iye ali ndi dzina limodzi limene anadzipatsa yekha.—Ekisodo 3:15.

  • Sikuti Mulungu ndi wosamvetsetseka, iye amafuna kuti timudziŵe.—Machitidwe 17:27.

  • Kudziŵa dzina la Mulungu ndi cinthu coyamba cimene mungacite kuti mukhale naye paubwenzi.—Yakobo 4:8.

Kodi n’kulakwa kuchula dzina la Mulungu?

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Inde

  • Iyai

  • Kaya

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA

“Usagwilitse nchito dzina la Yehova Mulungu wako mosasamala.” (Ekisodo 20:7) Kumakhala kulakwa ngati tiseŵenzetsa dzina la Mulungu mopanda ulemu.—Yeremiya 29:9.

ZINA ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA

  • Yesu anali kudziŵa dzina la Mulungu ndipo analiseŵenzetsa.—Yohane 17:25, 26.

  • Mulungu akutipempha kuseŵenzetsa dzina lake. —Salimo 105:1.

  • Adani a Mulungu amacititsa anthu kuti asadziŵe dzina lake.—Yeremiya 23:27.