Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YA PACIKUTO | MUNTHU AMENE MUMAKONDA AKAMWALILA

Kupilila Cisoni

Kupilila Cisoni

Pali malangizo ambili amene angathandize munthu kupilila cisoni. Koma si onse amene ndi othandiza. Mwacitsanzo, ena angakuuzeni kuti musalile kapena kuonetsa cisoni. Ena angakuuzeni kuti muonetse cisoni canu conse. Koma Baibulo limapeleka malangizo othandiza pankhaniyi. Malangizo ake ndi ogwilizana kwambili ndi zimene ofufuza apeza masiku ano.

M’zikhalidwe zina, anthu amakamba kuti mwamuna weniweni salila. Koma kodi tifunika kucita manyazi kulila tikakhala pagulu la anthu? Akatswili oona za matenda a m’maganizo anati, kulila ndi njila yabwino yoonetsela cisoni. M’kupita kwa nthawi, kulila kungakuthandizeni kupilila imfa ya wokondedwa wanu. Koma kubisa cisoni canu kungabweletse mavuto ambili. Baibulo silicilikiza mfundo yakuti mwamuna weniweni salila. Mwacitsanzo, ganizilani zimene Yesu anacita. Iye analila pamaso pa anthu pamene Lazaro bwenzi lake anamwalila, ngakhale kuti anali ndi mphamvu zoukitsa anthu.—Yohane 11:33-35.

Kukhala wokwiya ndi njila inanso yoonetsela cisoni, makamaka pa imfa ya mwadzidzidzi. Munthu wofeledwa amakhala wokwiya pa zifukwa zosiyanasiyana. Cifukwa cimodzi cingakhale cakuti, munthu amene amamulemekeza angakambe mau osathandiza kwenikweni. Mwamuna wina dzina lake Mike, amene akhala ku South Africa, anakamba kuti: “Atate anamwalila ndili ndi zaka 14. Tili pamalilo, m’busa wa chalichi ca Anglican anakamba kuti Mulungu amafuna anthu abwino ndipo amawatenga. * Zimenezi zinandikhumudwitsa cifukwa atate ndinali kuŵakonda kwambili. Ngakhale kuti papita zaka 63, ndimakhumudwabe.”

Nanga bwanji ngati mukudziimba mlandu? Pakacitika imfa ya mwadzidzidzi, wofeledwa angakhale ndi maganizo akuti, ‘Ndikanacita zakutizakuti, munthuyo sakanamwalila.’ Mwina nthawi yothela imene munaonana ndi munthuyo munasiyana maganizo. Zocitika ngati zimenezi zingacititse kuti muzidziimba mlandu.

Ngati mukudziimba mlandu kapena ndinu wokwiya cifukwa ca imfa ya wokondedwa wanu, musabise mmene mukumvelela. Fotokozelani mnzanu wapamtima amene angakumvetseleni ndi kukutsimikizilani kuti maganizo otelo amavutitsa ofeledwa ambili. Baibulo limati: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo ilo ndi m’bale amene anabadwila kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—Miyambo 17:17.

Bwenzi la pamtima limene anthu ofeledwa angakhale nalo ndi Mlengi wathu, Yehova Mulungu. Muuzeni zakukhosi kwanu m’pemphelo cifukwa iye “amakudelani nkhawa.” (1 Petulo 5:7) Kuonjezela apo, iye walonjeza onse amene amatelo kuti adzatsitsimula mtima ndi maganizo ao, cifukwa “mtendele wa Mulungu umaposa kuganiza mozama kulikonse.” (Afilipi 4:6, 7) Cinanso, lolani Mulungu kuti akuthandizeni kupilila cisoni kupitila m’Mau ake, Baibulo. Lembani m’ndandanda wa malemba otonthoza. (Onani  kabokosi) Mwina mungaloŵeze ena mwa malemba amenewo pamtima. Kuganizila malembawa mozama kungakuthandizeni kwambili makamaka usiku mukakhala nokha, ndiponso ngati mukulephela kugona.—Yesaya 57:15.

Mwamuna wina wa zaka 40 amene tam’patsa dzina lakuti Jack, mkazi wake anamwalila ndi matenda a kansa. Jack anakamba kuti nthawi zina amasungulumwa kwambili. Koma pemphelo lamuthandiza kwambili. Iye anati: “Kupemphela kwa Yehova kumandithandiza kuona kuti sindili ndekha. Kaŵilikaŵili, ndimauka pakati pa usiku ndipo ndimalephela kugonanso. Ndikaŵelenga ndi kuganizila mozama Malemba otonthoza, ndimauza Mulungu zakukhosi kwanga m’pemphelo. Ndikatelo, mtima wanga umakhala m’malo ndipo ndimakhala ndi mtendele wa m’maganizo. Izi zimandithandiza kupeza tulo.”

Mai a mtsikana wina dzina lake Vanessa, anamwalila atadwala kwambili. Iyenso waona kuti pemphelo limathandiza kwambili. Iye anati: “Panthawi yovutayi, ndinali kupemphela kwa Mulungu uku ndikulila. Yehova anamvetsela mapemphelo anga ndipo anandipatsa mphamvu zakuti ndipilile.”

Alangizi ena a anthu ofedwa amauza amene akuvutika ndi cisoni kuti azigwila nchito zothandiza ena. Kugwila nchito zotelo kumabweletsa cimwemwe ndipo kumacepetsa cisoni ca munthu. (Machitidwe 20:35) Ofedwa ambili amene ndi Akristu, aona kuti kugwila nchito zimenezi n’kotonthoza kwambili.—2 Akorinto 1:3, 4.

^ par. 5 Izi si zimene Baibulo limaphunzitsa. Baibulo limafotokoza zinthu zitatu zimene zimacititsa imfa.—Mlaliki 9:11; Yohane 8:44; Aroma 5:12.