Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YA PACIKUTO

Munthu Amene Mumakonda Akamwalila

Munthu Amene Mumakonda Akamwalila

“Mulungu akudziŵa zonse. . . . Usalile.”

Mau amenewa anaŵeleŵesedwa kwa mkazi wina dzina lake Bebe. Iye anali pamalilo a atate ake amene anafa pangozi ya galimoto.

Bebe anali kukonda kwambili atate ake. Bwenzi la banja lao ndilo linakamba mau amene ali pamwambapa, koma mauwo sanamutonthoze. Iye mobwelezabweleza anali kudziuza kuti: “Atate anafa imfa yoipa.” Patapita zaka, Bebe analemba za imfa ya atate ake m’buku. Izi zinaonetsa kuti anali akali ndi cisoni.

Malinga ndi zimene zinacitikila Bebe, zimatenga nthawi yaitali kuti munthu apilile cisoni makamaka ngati munthu amene anamwalila anali kum’konda kwambili. M’pomveka kuti Baibulo limacha imfa kuti “mdani womalizila.” (1 Akorinto 15:26) Imfa imasokoneza kwambili umoyo wathu, ndipo mwadzidzidzi imatenga anthu amene timakonda kwambili. Palibe amene angapewe zotsatilapo za imfa. Conco, n’zosadabwitsa kuti zimativuta kupilila imfa ndi zotsatilapo zake.

Mwina mumadzifunsa kuti: ‘Kodi cisoni cimatenga nthawi yaitali bwanji kuti cithe? Nanga munthu angapilile bwanji cisoni? Ndingatonthoze bwanji anthu amene okondedwa ao anamwalila? Kodi pali ciyembekezo ciliconse kaamba ka okondedwa athu amene anamwalila?’