Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi ndiyenera kudziwa zotani zokhudza malo ochezera a pa Intaneti?—Gawo 2

Kodi ndiyenera kudziwa zotani zokhudza malo ochezera a pa Intaneti?—Gawo 2

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi ndiyenera kudziwa zotani zokhudza malo ochezera a pa Intaneti?​—Gawo 2

Ikani manambala zinthu zotsatirazi, kuyambira ndi chinthu chimene mukuchiona kuti n’chofunika kwambiri.

․․․․․ zinthu zachinsinsi

․․․․․ nthawi yanga

․․․․․ mbiri yanga

․․․․․ anzanga

KODI pa zinthu zimene zili pamwambazi, ndi chiti chimene mukuona kuti n’chofunika kwambiri kwa inuyo moti mwachiika poyambirira? Ngati mumagwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti, muyenera kusamala ndi chinthu chimenecho, komanso zitatu zinazo.

Kodi mukuona kuti mukufunikiradi kukhala ndi malo ochezera a pa Intaneti? Ngati mudakali pakhomo pa makolo anu, iwo ndi amene ali ndi udindo wokusankhirani. * (Miyambo 6:20) Monga mmene zilili ndi Intaneti yonse, malo ochezera a pa Intaneti ali ndi ubwino komanso kuipa kwake. Ngati makolo anu akuona kuti simukufunikira kukhala ndi malo amenewa, muyenera kuwamvera.—Aefeso 6:1.

Komabe ngati makolo anu amakulolani kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti, kodi mungatani kuti muziwagwiritsa ntchito mwanzeru? Nkhani ya “Zimene Achinyamata Amadzifunsa” yomwe inatuluka m’Galamukani! ya July 2011, inafotokoza zinthu ziwiri, zokhudza kuika zinthu zachinsinsi pa Intaneti komanso kuchuluka kwa nthawi imene mumakhalapo. M’nkhani ino tikambirana mmene malowa amakhudzira mbiri yanu komanso anzanu amene mumapeza.

MBIRI YANU

Muyenera kusamala ndi zinthu zimene mumaika pa Intaneti n’cholinga choti muteteze mbiri yanu. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mwagula galimoto yatsopano yosaphwanyika paliponse. Kodi simungayesetse kuisamalira? Koma kodi mungamve bwanji ngati mutachita nayo ngozi chifukwa choyendetsa mosasamala?

Mofanana ndi zimenezi, mukhoza kuwononga mbiri yanu ngati mutamagwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti mosasamala. Mtsikana wina dzina lake Cara, ananena kuti: “Kulemba ndemanga kapena kuika chithunzi musanaganizire bwino pamalo ochezera a pa Intaneti, kukhoza kukuwonongerani mbiri yanu.” Mwachitsanzo, taganizirani mmene zinthu zotsatirazi zingakhudzire mbiri yanu.

Zithunzi zanu. Mtumwi Petulo analemba kuti: “Khalani ndi khalidwe labwino pakati pa anthu.” (1 Petulo 2:12) Ngati munaonapo zithunzi zimene anthu amaika pamalo ochezera a pa Intaneti, kodi mungati ndi zotani?

“Nthawi zina anthu amene ndimawalemekeza amapezeka kuti aika zithunzi zosonyeza kuti analedzera.”—Anatero Ana, wazaka 19.

“Atsikana ambiri amakonda kuika zithunzi zimene zimaonetsa kwambiri matupi awo. Ukawaona pamasom’paso sungakhulupirire kuti ndi omwe aja.”—Anatero Cara, wazaka 19.

Kodi mungaganize zotani ngati mutaona munthu wina ataika chithunzi pamalo ochezera a pa Intaneti chosonyeza (1) zovala zoonetsa thupi lake kapena (2) kuti waledzera?

1 ․․․․․

2 ․․․․․

Ndemanga zanu. Lemba la Aefeso 4:29 limati: “Mawu alionse owola asatuluke pakamwa panu.” Ena aona kuti anthu amakonda kunena mawu otukwana, miseche, komanso zinthu zolaula pamalo ochezera a pa Intaneti.

“Anthu ambiri amamasuka kwambiri akakhala pamalo ochezera a pa Intaneti. Munthu amatha kulemba mawu oti sangamasuke kuwanena pamasom’pamaso. Mwina simungalembe zinthu zotukwana, koma mwina zikhoza kukhala zokopana, zoderera ena, kapena zosakhala bwino.”—Anatero Danielle, wazaka 19.

Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani anthu ambiri amamasuka kwambiri akakhala pa Intaneti?

․․․․․

Kodi muyenera kuda nkhawa ndi zithunzi kapena zinthu zina zimene mumaika pa Intaneti? Inde, muyenera kuda nazo nkhawa. Mtsikana wina dzina lake Jane, anati: “Timaphunzira zimenezi kusukulu kwathu. Timakambirana zimene olemba ntchito amachita akafuna kudziwa bwino amene akufuna kumulemba ntchito poyang’ana malo ake ochezera a pa Intaneti.”

Dr. B. J. Fogg analemba m’buku lake kuti amachitanso zomwezo akafuna kulemba munthu ntchito. Iye anati: “Ndimaona kuti ndi udindo wanga kuchita zimenezi. Ndikaona zimene munthuyo amalemba pa Intaneti, n’kupeza kuti amalemba zopanda nzeru, sindimulemba ntchito. Ndimafuna kuti anthu amene ndikugwira nawo ntchito azikhala oganiza bwino.”

Ngati ndinu Mkhristu, muyeneranso kuganizira mmene zinthu zimene mumaika pa Intaneti zingakhudzire Akhristu anzanu komanso anthu ena. Tiyenera kutengera chitsanzo cha mtumwi Paulo, yemwe anati: “Sitikuchita chilichonse chokhumudwitsa.”—2 Akorinto 6:3; 1 Petulo 3:16.

Zimene Mungachite

Ngati makolo anu amakulolezani kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti, onaninso zithunzi zimene munaika pamalowa ndipo kenako dzifunseni kuti: ‘Kodi zithunzizi zikusonyeza kuti ndine munthu wotani? Kodi ndimafuna kuti anthu azindiona kuti ndine munthu wotere? Kodi sindingachite manyazi ngati makolo anga, akulu ku mpingo kwathu kapena munthu wofuna kundilemba ntchito ataona zithunzi zimenezi?’ Ngati mungachite manyazi, ndiye ndi bwino kuzichotsa. Zimenezi n’zimene mtsikana wina wazaka 21, dzina lake Kate, anachita. Iye ananena kuti: “Mkulu wa mumpingo mwathu anandilankhula ataona chithunzi chimene ndinaika pamalo anga ochezera a pa Intaneti. Ndinayamikira kwambiri malangizo amene anandipatsa chifukwa iye ankafuna kuti mbiri yanga isaipe.”

Onaninso ndemanga zimene mumalemba komanso ndemanga zimene anthu ena amakulemberani. Musamalekerere “nkhani zopusa kapena nthabwala zotukwana.” (Aefeso 5:3, 4) Mtsikana wina wazaka 19, dzina lake Jane, ananena kuti: “Nthawi zina anthu amatha kulemba ndemanga zoipa kapena mawu amene akhoza kukhala ndi matanthauzo awiri. Ngakhale kuti si iweyo amene walemba ndemangayo, imakuwonongerabe mbiri chifukwa chakuti ndemangayo yalembedwa pamalo ako.”

Choncho pa nkhani ya zithunzi komanso ndemanga zimene mumalemba pamalo anu a pa Intaneti, kodi mungadziikire malamulo otani kuti musaipitse mbiri yanu?

․․․․․

ANZANU AMENE MUMAPEZA

Ngati mukuyendetsa galimoto yanu, kodi mungangotenga munthu aliyense amene wakuimitsani? Ngati makolo anu amakulolezani kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti, muyenera kusankha bwino anthu ocheza nawo. Ndiye kodi mungasankhe bwanji anthu amenewo?

“Anthu ena amangokhala ndi cholinga choti akhale ndi anthu ambiri ocheza nawo. Amatha kuyamba kucheza ndi anthu omwe sakuwadziwa n’komwe.”—Anatero Nayisha, wazaka 16.

“Malo ochezera a pa Intaneti amachititsa kuti uyambenso kucheza ndi anthu amene unkacheza nawo kalekale. Koma nthawi zina zimakhala bwino kungowaiwala.”—Anatero Ellen, wazaka 25.

Zimene Mungachite

Yesani izi: Onaninso bwinobwino anzanuwo. Onani anzanu onse amene muli nawo pamalo ochezera a pa Intaneti ndipo ngati kungatheke chotsanipo anzanu ena. Mukamaunika mnzanu aliyense, dzifunseni kuti:

1. ‘Kupatula pa zimene anaika pamalo ake a pa Intaneti, kodi munthu ameneyu amachita zotani?’

2. ‘Kodi amaika zithunzi komanso ndemanga zotani?’

3. ‘Kodi munthu ameneyu ndi mnzanga wabwino?’

“Nthawi zambiri ndimaunikanso anzanga amene ndili nawo mwezi uliwonse. Ngati pali aliyense amene ndikumukayikira kapena sindikumudziwa bwino, ndimamuchotsa.”—Anatero Ivana, wazaka 17.

Yesani izi: Khazikitsani lamulo. Khazikitsani lamulo lokhudza anthu amene mungawapemphe kapena kuwavomereza kuti akhale anzanu. (1 Akorinto 15:33) Mwachitsanzo, mtsikana wina dzina lake Leanne, ananena kuti: “Ndimatsatira lamulo ili: Ngati munthu sindikumudziwa, sindivomera pempho lake loti akhale mnzanga. Ngati walemba kapena kuika zinthu zokayikitsa pamalo ake a pa Intaneti, ndimamuchotsa pamndandanda wa anzanga.” Anthu enanso akhazikitsa malamulo ofanana ndi amenewa.

“Sindingovomereza aliyense kuti akhale mnzanga, chifukwa anthu ena akhoza kukuika m’mavuto.”—Anatero Erin, wazaka 21.

“Anzanga ena amene ndinali nawo kusukulu akhala akundipempha kuti ndizicheza nawo pamalo anga a pa Intaneti. Koma ndili kusukulu ndinkayesetsa kuwapewa anthu amenewa, ndiye palibe chifukwa choti ndiyambe kucheza nawo panopa.”—Anatero Alex, wazaka 21.

Lembani m’munsimu malamulo amene muzitsatira posankha anthu ocheza nawo pa Intaneti.

․․․․․

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.dan124.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Galamukani! siilimbikitsa kapena kuletsa anthu kugwiritsa ntchito malo enaake ochezera a pa Intaneti. Akhristu ayenera kuonetsetsa kuti akugwiritsa ntchito Intaneti popanda kuphwanya mfundo za m’Baibulo.—1 Timoteyo 1:5, 19.

[Mawu Otsindika patsamba 10]

Baibulo limati: “Ndi bwino kusankha dzina labwino kusiyana ndi chuma chochuluka.”—Miyambo 22:1.

[Bokosi patsamba 12]

FUNSANI MAKOLO ANU

Kambiranani ndi makolo anu nkhaniyi komanso nkhani ngati yomweyi yomwe inatuluka mu Galamukani! ya July 2011. Kambiranani mmene kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti kukukhudzira (1) zinthu zanu zachinsinsi, (2) nthawi yanu, (3) mbiri yanu, ndi (4) anzanu amene mumapeza.

[Bokosi patsamba 13]

MAWU KWA MAKOLO

Mwina ana anu amadziwa zambiri zokhudza malo ochezera a pa Intaneti kuposa inuyo. Komabe iwo sangachite zinthu mwanzeru kuposa inuyo. (Miyambo 1:4; 2:1-6) Munthu wina woona za chitetezo cha pa Intaneti, dzina lake Parry Aftab, anati: “Ana amadziwa zambiri zokhudza zipangizo zamakono koma makolo amadziwa zambiri zokhudza moyo.”

M’zaka zaposachedwapa, malo ochezera a pa Intaneti afala kwambiri. Kodi mwana wanu wafika poti mungamulole kugwiritsa ntchito malo amenewa? Inu makolo ndi amene muli ndi udindo woona zimenezi. Mofanana ndi kuyendetsa galimoto, kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti kuli ndi mavuto ake. Kodi mavuto ena ndi otani?

ZINTHU ZACHINSINSI. Achinyamata ambiri sadziwa kuopsa koika zinthu zambirimbiri zokhudza iwowo pa Intaneti. Sadziwa kuti kulemba zinthu monga kumene amakhala, sukulu imene amaphunzira, nthawi imene amapezeka panyumba, n’koopsa chifukwa kukhoza kuika moyo wawo komanso wa banja lawo pa ngozi.

Zimene mungachite. Ana anu ali aang’ono munawaphunzitsa kuti aziyang’ana mbali zonse ziwiri akamaoloka msewu. Ndipo popeza kuti panopa akula, muyenera kuwaphunzitsa mmene angamagwiritsire ntchito Intaneti mwanzeru. Werengani malangizo okhudza kuika zinthu zachinsinsi pa Intaneti m’nkhani ya “Zimene Achinyamata Amadzifunsa” imene inatuluka mwezi watha. Onaninso Galamukani! ya October 2008, tsamba 3 mpaka 9. Kenako kambiranani nkhanizo ndi ana anu. Yesetsani kuphunzitsa ana anu kukhala ndi “nzeru zopindulitsa ndiponso kuganiza bwino” pa nkhani yogwiritsa ntchito Intaneti.—Miyambo 3:21.

NTHAWI. Anthu ambiri amati akayamba kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti, amafika poti safuna kuchokapo. Mnyamata wina wazaka 23, dzina lake Rick, anati: “Patangopita masiku ochepa kuchokera pamene ndinakhala ndi malo ochezera a pa Intaneti, sindinkafuna kuchokapo. Ndinkangokhalira kuona zithunzi komanso ndemanga zimene anzanga alemba.”

Zimene mungachite. Werengani pamodzi ndi ana anu nkhani yakuti “Zimene Achinyamata Amadzifunsa—Kodi ndimagwiritsira ntchito foni, TV, kompyuta kapena Intaneti mopitirira malire?” yomwe inatuluka mu Galamukani! ya January 2011. Onani makamaka patsamba 26. Thandizani ana anu kuti ‘asamachite zinthu mopitirira malire’ komanso kuti asamakhale pa Intaneti nthawi yaitali kwambiri. (1 Timoteyo 3:2) Muzikumbutsa ana anu kuti pali zinthu zinanso zofunika kwambiri kupatula pa kugwiritsa ntchito Intaneti.

MBIRI YANU. Baibulo limati: “Mnyamata amadziwika ndi ntchito zake, ngati zochita zake zili zoyera ndiponso zowongoka.” (Miyambo 20:11) Zimenezi ndi zoona pa nkhani yogwiritsa ntchito Intaneti. Komanso popeza kuti zinthu zimene zaikidwa pa Intaneti zimaonedwa ndi anthu ambiri, zimene ana anu angaikepo zingakhudze mbiri ya banja lanu.

Zimene mungachite. Ana anu ayenera kudziwa kuti zimene amaika pa Intaneti zimakhudza mbiri yawo. Komanso ayenera kumvetsa mfundo yakuti zimene zimaikidwa pa Intaneti, zimakhala pamenepo mpaka kalekale. Dr.  Gwenn Schurgin O’Keeffe analemba m’buku lake kuti: “Nkhani yakuti zinthu zimene zimaikidwa pa Intaneti zimakhala pomwepo mpaka kalekale ndi yovuta kwa achinyamata kuimvetsa, koma ndi yofunika kuidziwa. Njira imodzi yowathandizira kumvetsa zimenezi ndi kuwauza kuti asamalembepo zinthu zimene sangamasuke kuuza munthu wina pamasom’pamaso.”—CyberSafe.

ANZAWO AMENE AMAPEZA. Mtsikana wina wazaka 23, dzina lake Tanya, anati: “Achinyamata ambiri amafuna kutchuka, choncho amalola kukhala ndi anzawo ambirimbiri osawadziwa komanso opanda khalidwe.”

Zimene mungachite. Thandizani mwana wanu kukhazikitsa lamulo loti azitsatira akakhala pa Intaneti. Mwachitsanzo, mtsikana wina wazaka 22, dzina lake Alicia, ananena kuti iye sakonda kuvomereza kuti anzawo a anthu amene amacheza nawo akhalenso anzake. Iye anati: “Ngati munthuyo sindimudziwa komanso sindinakumanepo naye pamasom’pamaso, sindimulola kuti akhale mnzanga. Sindifuna kungovomereza munthu winawake chifukwa chakuti amacheza ndi munthu amene inenso ndimacheza naye.”

Bambo wina, dzina lake Tim, ndi mkazi wake Julia, anakhazikitsa malo awo ochezera a pa Intaneti ndi cholinga choti azidziwa anthu amene mwana wawo akucheza nawo. Julia anati: “Tinapempha mwana wathuyo kuti atiike pa mndandanda wa anthu amene amacheza nawo. Timaona kuti anthu amene amacheza nawo pa Intaneti ali ngati anzake amene amabwera nawo kunyumba kwathu. Choncho, timafuna kuwadziwa bwinobwino.”

[Chithunzi patsamba 11]

Ngati mukuyendetsa galimoto mosasamala mukhoza kuchita ngozi. Chimodzimodzinso ndi mbiri yanu. Ikhoza kuwonongeka ngati mumaika zithunzi kapena ndemanga zolakwika pamalo anu ochezera a pa Intaneti

[Chithunzi patsamba 12]

Ngati muli pa galimoto, kodi mungatenge munthu aliyense amene akukuimitsani? N’chimodzimodzinso ndi anzanu a pa Intaneti, si bwino kumangolola aliyense kuti akhale mnzanu