Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumasankha Nyimbo Mwanzeru?

Kodi Mumasankha Nyimbo Mwanzeru?

Kodi Mumasankha Nyimbo Mwanzeru?

“Nyimbo zimene makolo anga amakonda sizindisangalatsa ngakhale pang’ono,” anatero Jordan, wazaka 17. *

“Nyimbo zimene mwana wanga amakonda kumvera zimamuchititsa kuti azingokhala wolusa komanso wokhumudwa,” anatero mayi ake a mnyamatayu, a Denise.

N’CHIFUKWA chiyani nthawi zambiri makolo ndi ana awo sagwirizana pa nkhani ya nyimbo? Chifukwa chimodzi ndi chakuti zokonda za munthu zimasintha akamakula. Chifukwa chinanso n’chakuti nyimbo nazonso zimasinthasintha. N’chifukwa chake nyimbo imene anthu angaikonde lero, ikhoza kufwifwa pofika mawa.

Komabe mfundo ndi yakuti nyimbo zimatikhudza kwambiri. Kodi munayamba mwamverapo nyimbo inayake n’kukupangitsani kusangalala kapena kukhumudwa? Nthawi zina, Mfumu Sauli ya Isiraeli ikamavutika maganizo, inkapeza bwino ikamvetsera nyimbo. (1 Samueli 16:23) Nyimbo tingaziyerekezere ndi anthu amene timacheza nawo. Ena angatichititse kuti tizisangalala komanso kuti tikhale ndi makhalidwe abwino monga chikondi, pamene ena angatichititse kuti tizingokhala okhumudwa komanso tizidana ndi anthu.—Miyambo 13:20.

Ndiye popeza kuti nyimbo zimakhudza kwambiri khalidwe lathu, makolo ndiponso ana ayenera kuyesetsa kusankha nyimbo mwanzeru. Kodi makolo mumadziwa nyimbo zimene ana anu amamvera komanso kuchuluka kwa nthawi imene amamvera nyimbozo? Ndipo kodi inuyo mumawathandiza ana anu kusankha bwino nyimbo?

Dziwani kuti kungoletsa ana anu kumvera nyimbo za mtundu winawake si kokwanira. Muyenera kuwathandiza kupeza nyimbo zabwino zimene angamamvetsere. Buku lina linanena kuti: “Ngati mwaletsa munthu chinthu chimene amachikonda kwambiri, muyenera kumupatsa chinthu china cholowa m’malo, apo ayi akatenganso chimene mwamuletsacho.”—On Becoming Teenwise.

Mfundo ina imene muyenera kuiganizira ndi yokhudza kuchuluka kwa nthawi imene ana anu amathera akumvera nyimbo. Kodi nthawi zina amamvera nyimbo m’malo mochita zinthu zofunika kwambiri monga homuweki, zinthu zauzimu, kapena ntchito zapakhomo? Kumbukirani kuti Baibulo limati: “Chilichonse chili ndi nthawi yake.”—Mlaliki 3:1.

Nyimbo zikhoza kutichititsanso kuti tizidzipatula. Ndi zoona kuti nthawi zina timafunika kukhala patokha kuti tizisinkhasinkha. (Salimo 1:2, 3) Koma kuchita zimenezi mopitirira malire si bwino chifukwa kumachititsa kuti munthu akhale wodzikonda. (Miyambo 18:1) Mwachitsanzo, Felipe, yemwe panopa ali ndi zaka 20, ankaona kuti munthu aliyense sayenera kumusokoneza akamamvera nyimbo. Iye anati: “Koma amayi anga ankada nkhawa kwambiri chifukwa ndinkakonda kukhala ndekha.”

Kodi n’chiyani chingathandize achinyamata, monga Felipe, ndi makolo awo kupewa kukangana pa nkhani ya nyimbo? Kodi tonsefe tingasankhe bwanji nyimbo zabwino? Mfundo za m’Baibulo zathandiza anthu ambiri kuti azisankha bwino nyimbo. Makolo, mungachite bwino kukambirana mafunso atatu otsatirawa ndi ana anu.

Uthenga wake ndi wotani? Baibulo limati: “Dama ndi chonyansa chamtundu uliwonse kapena umbombo zisatchulidwe n’komwe pakati panu.” (Aefeso 5:3) Nyimbo zambiri zimakhala ndi mawu abwinobwino. Koma nyimbo zina zimafunika kusamala nazo chifukwa zimatha kukhala ndi mawu olimbikitsa makhalidwe amene sagwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Mitundu ina ya nyimbo imalimbikitsa zinthu zachiwerewere, zachiwawa komanso chidani. Munthu wina wolemba mabuku, dzina lake Karen Sternheimer, anati: “Nthawi zambiri nyimbo za rap zimakhala ndi mawu olimbikitsa nkhanza, onyoza akazi komanso otukwana.” Nazonso nyimbo za heavy metal zimalimbikitsa zachiwawa komanso zamatsenga. Ndipo nyimbo zina zotchuka zooneka ngati zabwinobwino zikhoza kukhala ndi mawu enaake amene amalimbikitsa makhalidwe oipa. Choncho, mukamasankha nyimbo, muzigwiritsa ntchito “luntha la kuganiza.” (Aroma 12:1) Musamangotengeka ndi nyimbo zimene anthu ambiri akuzikonda kapena zimene zikumveka bwino.

Kodi nyimboyo imandikhudza bwanji? Baibulo limati: ‘Uteteze mtima wako, pakuti mumtimamo ndiye muli akasupe a moyo.’ (Miyambo 4:23) Anthu ena akhoza kudziwa kuti ndinu munthu wotani poona nyimbo zimene mumamvetsera. Koma si zokhazo; nyimbo zimene mumamvera zimasinthanso mmene mumachitira zinthu. Jordan amene tinamutchula uja ananena kuti: “Nyimbo zina zimene ndinkamvetsera zinkandichititsa kuti ndizikhala wolusa.” Dzifunseni kuti: ‘Kodi nyimbo zimene ndimakonda zimakhudza bwanji moyo wanga? Kodi ndikamvetsera nyimbozo ndimaona kuti ndatsitsimulidwa, kapena zangondichititsa kukhala wokhumudwa? Kodi zimandichititsa kuyamba kuganizira zinthu zolakwika?’ (Akolose 3:5) Ngati nyimbo zinazake zimakuchititsani kuganizira zinthu zolakwika, muyenera kusiya kuzimvera. (Mateyu 5:28, 29) Mtsikana wina wazaka 17, dzina lake Hannah, ananena kuti: “Ndimaona kuti kumvera nyimbo zoipa kumawononga makhalidwe a munthu, choncho sindifuna kuzimvera ngakhale pang’ono.”

Kodi nyimbo zingasinthe khalidwe langa? Lemba la Amosi 5:15 limati: “Danani ndi choipa ndipo muzikonda chabwino.” Kuchita zimenezi n’kovuta kwambiri masiku ano chifukwa, mogwirizana ndi zimene Baibulo linalosera, anthu ambiri ndi “odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika, osakonda achibale awo, osafuna kugwirizana ndi anzawo, onenera anzawo zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, . . . okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.” (2 Timoteyo 3:1-4) N’chifukwa chake vesi 5 limanena kuti: “Anthu amenewa uwapewe.”

Kodi mungapewe bwanji anthu amenewa? Kungopewa kucheza nawo sikokwanira, muyeneranso kupewa zinthu zoipa zimene amafalitsa. (Aefeso 4:25, 29, 31) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti simungakhale ndi nyimbo zambiri zomvetsera? Ayi, pali nyimbo zambiri zabwino zimene mungamvetsere.

Muzimvera Nyimbo Zosiyanasiyana

M’mabanja ambiri, makolo amamvetsera nyimbo zimene ana awo amakonda, ndipo ana nawonso amamvetsera nyimbo zimene makolo awo amakonda. Mwachitsanzo, mayi wina dzina lake Lena, ananena kuti: “Ndinayamba kumvera nyimbo zimene mwana wanga wazaka 13 amakonda ndipo panopa nanenso ndimazikonda.” Komanso mtsikana wina wazaka 16, dzina lake Heather, amabwerekana ma CD a nyimbo ndi makolo ake.

Padziko lonse, anthu mamiliyoni ambiri a Mboni za Yehova ochokera m’zikhalidwe zosiyanasiyana, achikulire komanso achinyamata, amamvera nyimbo zamitundu yosiyanasiyana, kuphatikizapo nyimbo zauzimu za m’buku la Imbirani Yehova. * Iwo amachita zimenezi ngakhale kuti m’mayiko ena nyimbo za m’bukuli zimasiyana ndi zimene amakonda kumvetsera kwawoko.

Kaya ndinu kholo kapena wachinyamata, musanagule nyimbo kapena kuzikopera pa Intaneti, mungachite bwino kudzifunsa mafunso awa: ‘Kodi ndani anandipatsa mphatso yoti ndizisangalala ndi nyimbo? Kodi si Mlengi wanga Yehova Mulungu? Ndiye kodi ndingasonyeze bwanji kuti ndimayamikira mphatso imene iye anandipatsa? Kodi sindiyenera kusonyeza kuyamikira posankha nyimbo zogwirizana ndi mfundo zake?’ Kudzifunsa mafunso amenewa kungakuthandizeni kusankha nyimbo mwanzeru, zomwe zingachititse kuti inuyo musangalale komanso musangalatse mtima wa Mlengi wanu.—Miyambo 27:11.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Tasintha mayina ena m’nkhaniyi.

^ ndime 17 Mukhoza kukopera nyimbozi pa Intaneti pa adiresi iyi: www.dan124.com.

[Mawu Otsindika patsamba 7]

Nyimbo zina zimalimbikitsa makhalidwe oipa

[Mawu Otsindika patsamba 8]

Pali nyimbo zambiri zabwino zimene mungamamvetsere

[Bokosi patsamba 7]

Chimene Chinachititsa Kuti Ndisinthe

Mnyamata wina wazaka 24, dzina lake Ashley, anati: “Ndili wamng’ono ndinkakonda kuledzera, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, komanso kuchita zachiwawa. Ndinkachita zimenezi chifukwa chakuti ndinkakonda kumvera nyimbo za heavy metal ndi rap. Nyimbozi zimakhala ndi mawu otukwana ndiponso olimbikitsa udani. Ndipo chifukwa chakuti zimakhala zaphokoso, ndikazimvetsera zinkandipatsa mphamvu zinazake. Nyimbozi zinandichititsa kuti ndizicheza ndi anthu amene amagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Komanso tinayamba kutengera makhalidwe oipa a anthu oimba nyimbozi.

“Koma pasanapite nthawi yaitali, zinthu zinafika poipa. Nthawi ina ndili ndi zaka 17, ndinamwa mankhwala ambiri osokoneza bongo, moti ndinatsala pang’ono kufa. Nditatsitsimuka, ndinapemphera kwa Mulungu kuti andithandize kusintha zochita zanga. Ndinakumbukira kuti mnyamata winawake anandiuza kuti dzina la Mulungu ndi Yehova. Ndinazindikira kuti a Mboni za Yehova ndi amene amaphunzitsa za Yehova, choncho ndinafufuza nambala yawo n’kuwaimbira foni. Ndipo kenako anayamba kundiphunzitsa Baibulo.

“Ndinasintha khalidwe langa ndiponso ndinasiya kumvera nyimbo zimene ndinkazikonda. Koma tsiku lina ndikutaya ma CD anga a nyimbo, mtima wina unkandiletsa moti ndinangoima pomwepo n’kumangowayang’ana. Kenako ndinadziuza kuti nyimbo zimenezi n’zimene zikundiwononga. Ndiye ndinatembenuka n’kumapita.

“Ngakhale kuti papita zaka zambiri kuchokera nthawi imeneyo, ndimakopekabe ndi nyimbo za heavy metal ndi rap. Choncho, ndimayesetsa kuzipeweratu chifukwa m’maganizo mwanga sindizisiyanitsa ndi mankhwala osokoneza bongo. Panopa ndimakonda kumvera nyimbo zabwino zosiyanasiyana, monga zachikondi komanso zina zosachita phokoso kwambiri. Koma chosangalatsa kwambiri n’chakuti panopa nyimbo sizindilepheretsa kuchita zinthu zofunika kwambiri.”

[Bokosi patsamba 9]

Malangizo kwa Makolo

Kodi nyimbo zimene mwana wanu amamvera zimakudetsani nkhawa? Kodi mungamuthandize bwanji kuti azimvera nyimbo zabwino popanda kumukhumudwitsa? Taonani malangizo otsatirawa:

Zidziweni bwino nyimbozo Musanamulankhule, fufuzani kaye. Mvetserani nyimbozo kuti mumvetse uthenga wake. Komanso onani zimene zalembedwa pa ma CD ake. Dzifunseni kuti, ‘Kodi pali chifukwa chodera nkhawa kapena ineyo ndikungovuta chabe?’ Baibulo limati: “Anthu anzeru amaganiza kaye asanalankhule, ndipo zimene amalankhula zimakhala zosangalatsa.”—Miyambo 16:23, Today’s English Version.

Chitani zinthu mwanzeru Nyimbo zimene mwana wanu amamvera, zingakuthandizeni kudziwa zimene zili mumtima mwake. Yesetsani kuzindikira mmene akumvera. Mufunseni kuti: “N’chifukwa chiyani umakonda nyimbo zimenezi? Kodi umamvera nyimbo zimenezi chifukwa cha nkhawa zinazake?” Ndiyeno mvetserani mwatcheru akamakuyankhani. Lemba la Miyambo 20:5 limati: “Maganizo a mumtima mwa munthu ali ngati madzi akuya, koma munthu wozindikira ndi amene amawatunga.”

Khalani ndi cholinga chomuthandiza Musangomuletsa nyimbozo. Muthandizeni ‘kugwiritsa ntchito mphamvu zake za kuzindikira, kuti azisiyanitsa choyenera ndi chosayenera.’ (Aheberi 5:14) Muphunzitseni mfundo imene ingamuthandize moyo wake wonse: M’phunzitseni kuti azitha kufufuza nkhani ndi kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo. Kuchita zimenezi kungathandize mwana wanu kuti azisankha zinthu mwanzeru komanso kuti azitsatira malangizo a m’Baibulo, omwe ndi ofunika kwambiri kuposa golide.—Miyambo 2:10-14; 3:13, 14.

Muuzeni mwachifundo ndi mokoma mtima zoyenera kuchita Baibulo limati: “Valani chifundo chachikulu, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima.” (Akolose 3:12) Mukamalankhula ndi mwana wanu musakhale wokakamira zinthu komanso womangofuna kukangana. Muzikumbukira kuti inunso munakhalapo mwana.

[Chithunzi patsamba 8]

Muzisankha nyimbo mwanzeru