Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafuta a Nyama Zam’madzi

Mafuta a Nyama Zam’madzi

Kodi Zinangochitika Zokha?

Mafuta a Nyama Zam’madzi

● Nyama zina zam’madzi monga ma dolphin zimathamanga mpaka kufika pa liwiro la makilomita pafupifupi 40 pa ola limodzi. Palinso mtundu wina wa anangumi umene umathamanga mpaka kufika makilomita 56 pa ola limodzi. Kwa zaka zambiri, asayansi sankamvetsa chimene chimachititsa kuti nyamazi zizithamanga kwambiri chonchi, chifukwa ankaona kuti zilibe mnofu wamphamvu kwenikweni. Koma chinsinsi cha nyamazi chagona pa mafuta amene amapezeka pansi pa khungu lawo.

Taganizirani izi: Mafutawa amakuta thupi lonse la nyamazo ndipo “analumikizidwa mwapadera ndi mitsempha ku mafupa.” (New World Encyclopedia) Mitsempha imeneyi inapangidwa ndi mapulotini enaake amene amapezekanso m’mafupa ndi mkati mwa khungu. Choncho mafuta amenewa si mafuta wamba.

Koma kodi mafuta amenewa amathandiza bwanji nyama zam’madzi monga ma dolphin ndi anangumi kuti zizithamanga kwambiri? Choyamba, mafutawa amachititsa kuti nyamazi zikhale ndi thupi loti lisamavutike kuyenda m’madzi. Chachiwiri, mafuta amene amapezeka m’zipsepse ali ndi timaulusi tolowanalowana komanso mapulotini, zimene zimachititsa kuti mchira uzipindika mosavuta komanso nyamazi zisamatope msanga. Mafutawa amagwira ntchito ngati sipuling’i: Minofu ikakokera mchirawo kumbali ina, mafutawo ndi amene amachititsa kuti mchirawo ubwerere msangamsanga.

Mafutawo amathandizanso kuti nyamazo ziziyandama komanso kuti zizimva kutentha. Komanso pa nthawi imene nyamazi zasowa chakudya, mafutawa amathandiza kuti zisafe ndi njala. M’pake kuti akatswiri ataganizira mmene mafutawa amagwirira ntchito, aona kuti akhoza kupanga sitima za pamadzi zothamanga kwambiri komanso zosawononga mafuta.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti nyamazi zikhale ndi mafuta ogwira ntchito mogometsa chonchi, kapena ndi umboni wakuti zinachita kulengedwa?

[Chithunzi patsamba 17]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Timaulusi

Mapulotini komanso tinthu tolowanalowana tokhala ngati timaulusi