Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kutulutsa Nyimbo Yabwino Kwambiri

Kutulutsa Nyimbo Yabwino Kwambiri

Kutulutsa Nyimbo Yabwino Kwambiri

MASIKU ano oimba achuluka ndipo pali mpikisano waukulu wotulutsa nyimbo zabwino kwambiri. Ngakhale nyimbo itakhala yabwino bwanji, m’kupita kwa nthawi imafwifwa ndipo anthu amasiya kuikonda. Nyimbo ndi zipangizo zakale zikulowedwa m’malo ndi zatsopano. Munthu wina wodziwa bwino nkhani za nyimbo, dzina lake Kelli S. Burns, ananena kuti makampani amene amathandiza oimba “nthawi zonse amasakasaka nyimbo imene anthu ambiri angaikonde.” Koma kuti munthu ajambule nyimbo yoti anthu aikonde, si nkhani yamasewera. Buku lina linanena kuti: “Ana ambiri amalota atadzakhala akatswiri oimba, . . . koma nthawi zambiri zimene amalakalakazo sizichitika, chifukwa pamakhala chintchito kuti munthu atulutse nyimbo yoti anthu n’kuikonda.”—Onani bokosi lakuti “Zinthu Zasintha Kwambiri pa Nkhani Yojambula Nyimbo,” patsamba 6.

Kupeka Nyimbo

Anthu opeka nyimbo (1) amasankha mawu okhudza mtima, ogwirizana ndi zimene anthu amakonda komanso kulakalaka pa moyo wawo. Kodi anthu amakonda kupeka nyimbo zotani? Ambiri amakonda kupeka nyimbo zachikondi. Anthu opeka nyimbo amayesetsanso kusankha mawu okopa oti munthu akangowamva asawaiwale.

Akamaliza, amayeserera kujambula nyimboyo kuti aone kuti ikumveka bwanji. Ngati kampani yojambula nyimbo yaona kuti nyimboyo ikhoza kuyenda malonda, amagwirizana zopitiriza kuijambula  (2). Koma ngati akumukayikira woimbayo (mwachitsanzo ngati si wotchuka), amatha kungogula nyimbo yakeyo n’kuuza woimba wodziwika kuti aiimbe.

Ku Situdiyo

Makampani ojambula nyimbo nthawi zambiri amaitana katswiri woti adzayang’anire ntchito yojambula nyimbo (3). Katswiriyo ndi amene amavomereza kuti nyimboyo ili bwino kapena isinthidwe mwina ndi mwina. Iye amasankhanso situdiyo yabwino imene angakajambulireko nyimboyo, oimba, ma injiniya komanso zida zimene zingafunike kuti nyimboyo imveke bwino komanso kuti anthu akaikonde.

Nthawi zambiri akamajambula nyimbo, amajambula chida chilichonse pachokhapachokha. Amayamba kujambula ng’oma, magitala ndi kiyibodi. Kenako, amajambula mawu ndiponso zinthu zina zokometsera kuti atulutse nyimbo yomveka bwino kwambiri (4).

Pamsika

Kuti nyimbo iyende malonda, makampani ojambula nyimbo amapanga mavidiyo a nyimbo  (5). Mavidiyowa amakhala aatali kuyambira pa mphindi zitatu mpaka zisanu. Anthu akamaonera mavidiyo amenewa, amakhala ngati akuona woimbayo pamasom’pamaso. Mavidiyowa amawapangira ndalama zambiri komanso amathandiza kuti anthu ambiri amudziwe woimbayo.

Oimba amagulitsa nyimbo zambiri akapita kokaimba (6). Choncho anthu amadziwa kuti kwatuluka nyimbo zatsopano chifukwa cha maulendo okaimba amenewa. Oimba ambiri amakhalanso ndi malo awo a pa Intaneti (7) amene amaikapo nyimbo, zithunzi, mavidiyo, ndemanga zawo ndiponso nkhani zokhudza nyimbo zimene aimbe kumalo osiyanasiyana. Anthu enanso amalemba ndemanga zawo pamalo amenewa. Malowa amasonyezanso malo osiyanasiyana a zisangalalo komanso malo a pa Intaneti omwe anthu angagulepo nyimbo.

Kodi ndani amasankha kuti nyimboyi ndi yabwino? Omvera ndi amene amasankha. Ndiye kodi n’chiyani chimakuchititsani inuyo kukonda nyimbo inayake? Kodi ndi mmene ikumvekera, woimba wake kapena pali mfundo zina zimene mumatsatira musanasankhe nyimbo? Mungachite bwino kudzifunsa mafunso amenewa chifukwa ngati mutapanda kusankha bwino, nyimbo zikhoza kukusokonezani. Zimenezi zikutikumbutsa malangizo ofunika kwambiri ochokera kwa Mlengi wathu, akuti: “Uteteze mtima wako kuposa zonse zimene ziyenera kutetezedwa, pakuti mumtimamo ndiye muli akasupe a moyo.”—Miyambo 4:23.

Kodi mungagwiritse ntchito bwanji malangizo anzeru amenewa posankha nyimbo? Ndipo ngati ndinu kholo, kodi mungatani kuti ana anu asamamvetsere nyimbo zimene zingawasokoneze?

[Bokosi patsamba 6]

Zinthu Zasintha Kwambiri pa Nkhani Yojambula Nyimbo

Kubwera kwa Intaneti komanso zipangizo zamakono zojambulira nyimbo kwachititsa kuti zinthu zipite patsogolo pa nkhani ya nyimbo. Masiku ano, oimba ambiri amatha kujambula nyimbo zapamwamba kwambiri ali kunyumba kwawo n’kuziika pa Intaneti, pomwe anthu padziko lonse angazimvetsere. Magazini ya The Economist inanena kuti “oimba ena otchuka amajambula ndiponso kufalitsa nyimbo zawo popanda kupita ku makampani ojambula nyimbo.”