Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nyimbo Ndi Mphatso

Nyimbo Ndi Mphatso

Nyimbo Ndi Mphatso

KODI mukuganiza kuti moyo ukanakhala wotani popanda nyimbo? Kodi bwenzi tikusangalala popanda kumvera tinyimbo tokoma totonthozera ana, nyimbo zachikondi zoimbidwa mwachifatse, ndi nyimbo zina zotenga mtima zoimbidwa ndi zida zamakono? Ambiri angaone kuti moyo wotere ungakhale wotopetsa ndi wosasangalatsa.

Kunena zoona, nyimbo zimatikhudza kwambiri chifukwa zimatifika pamtima. Zimatitonthoza, zimatigalamutsa, zimatipatsa mphamvu, komanso zimatisangalatsa. N’chifukwa chiyani nyimbo zimatikhudza kwambiri chonchi? Yankho lake ndi losavuta: Nyimbo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. (Yakobo 1:17) Choncho, tiyenera kuyamikira kwambiri mphatso imeneyi. Ndipo kaya ndinu mwana kapena wamkulu mukhoza kusangalala ndi nyimbo zosiyanasiyana.

Nyimbo zinayamba kale kwambiri. Mwachitsanzo, zinthu zimene akatswiri ofukula zinthu zakale apeza zimasonyeza kuti kuyambira kale kwambiri anthu a ku Africa ankaimba ng’oma, malipenga ndiponso mabelu. Nawonso anthu a ku China ankaimba tizitoliro tinatake. Anthu a ku Egypt, India, Israel ndi Mesopotamia ankaimba azeze. Koma mwina nkhani yakale kwambiri yodziwika bwino yokhudza nyimbo ndi imene imapezeka m’Baibulo pa Genesis 4:21. Lembali limanena kuti munthu wina dzina lake Yubala “anali tate wa onse oimba zeze ndi chitoliro.” Kenako patapita zaka zambiri, Mfumu Solomo ya Isiraeli, yomwe inkakonda kwambiri nyimbo, inaitanitsa matabwa abwino kwambiri opangira zida zoimbira monga azeze ndi zoimbira za zingwe.—1 Mafumu 10:11, 12.

Nthawi imeneyo, kuti mumvetsere nyimbo mukanafunikira kukhala ndi luso loimba kapena kukhala ndi mnzanu amene amadziwa kuimba. Koma masiku ano, nyimbo zili paliponse. Mukhoza kupeza mtundu uliwonse wa nyimbo pa Intaneti n’kuziika m’kachipangizo koti mukhoza kungokaika m’thumba n’kumamvetsera. Kafukufuku wina yemwe anachitika m’chaka cha 2009 ku Ulaya anasonyeza kuti achinyamata azaka zapakati pa 8 ndi 18, amatha maola oposa awiri tsiku lililonse akumvetsera nyimbo ndi zinthu zina.

Choncho n’zosadabwitsa kuti nyimbo ndiponso zipangizo zina zamakono zikuyenda malonda. Ndipotu nyimbo ndi bizinezi yotentha kwambiri. Koma kodi mumadziwa chimene chimachititsa kuti nyimbo inayake izikondedwa kwambiri?

[Bokosi/Chithunzi patsamba 3]

Kupeza Nyimbo pa Intaneti

KUKOPA: Nthawi zambiri munthu akakopa nyimbo pa Intaneti amalipira ndipo kenako nyimboyo imakhala yake. Ena amalembetsa kuti azikopa kapena kumvetsera nyimbo pa Intaneti kwaulere kwa miyezi ingapo, makamaka akagula foni kapena chinthu chinachake.

KUMVETSERA: Nthawi zina anthu amatha kumvetsera nyimbo pa Intaneti popanda kuzikopera mu kompyuta yawo kapena pa chinthu china chilichonse. Nthawi zambiri nyimbo zotere zimakhala zaulere, ngakhale kuti nthawi zina pamafunika kulembetsa kuti muzimvetsera nyimbozo.

[Tchati/Zithunzi patsamba 3]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Mmene Zinthu Zakhala Zikusinthira pa Nkhani ya Nyimbo

M’ma 1880

Galamafoni

M’ma 1890

Mawaya

M’ma 1940

Zimbale za gumbagumba

M’ma 1960

Makaseti

M’ma 1980

Ma CD

M’ma 1990

Ma MP3, AAC, WAV, ndi zina zotero.